Yobu atchulira mabwenzi ake matsoka ake, napempha amchitire chifundo. Adzitonthoza ndi Mpulumutsi wake
1 Koma Yobu anayankha, nati,
2 Mudzasautsa moyo wanga kufikira liti,
ndi kundithyolathyola nao mau?
3 Kakhumi aka mwandichititsa manyazi;
mulibe manyazi kuti mundiumira mtima.
4 Ndipo ngati ndalakwa ndithu,
kulakwa kwanga kuli ndi ine ndekha.
5 Ngati inu mudzikuza ndithu pa ine,
ndi kunditchulira mtonzo wanga kuti munditsutse nao.
6 Dziwani tsopano kuti Mulungu wandikhotetsera mlandu wanga,
nandizinga ndi ukonde wake.
7 Taonani, ndifuula kuti, Chiwawa! Koma sandimvera;
ndikuwa, koma palibe chiweruzo.
8 Iye ananditsekera njira kuti ndisapitireko,
naika mdima poyendapo ine.
9 Anandivula ulemerero wanga,
nandichotsera korona pamutu panga.
10 Nandigamula ponsepo, ndipo ndamukatu;
nachizula chiyembekezo changa ngati mtengo.
11 Wandiyatsiranso mkwiyo wake,
nandiyesera ngati wina wa adani ake.
12 Ankhondo ake andidzera pamodzi, nandiundira njira yao,
nandimangira misasa pozinga hema wanga.
13 Iye anandichotsera abale anga kutali,
ndi odziwana nane andiyesa mlendo konse.
14 Anansi anga andisowa,
ndi odziwana nane bwino andiiwala.
15 Iwo a m’nyumba mwanga ndi adzakazi anga andiyesa mlendo;
ndine wachilendo pamaso pao.
16 Ndikaitana kapolo wanga, sandibwezera mau,
chinkana ndimpembedza pakamwa panga.
17 Mpweya wanga unyansira mkazi wanga,
chinkana ndinampembedza ndi kutchula ana a thupi langa.
18 Angakhale ana aang’ono andipeputsa,
ndikanyamuka, andinena;
19 mabwenzi anga enieni onse anyansidwa nane;
ndi onse ndakondana nao asandulika adani anga.
20 Fupa langa laumirira pa khungu langa ndi mnofu wanga,
ndipo ndapulumuka ndili nazo nkhama za mano anga.
21 Ndichitireni chifundo, ndichitireni chifundo, mabwenzi anga inu;
pakuti dzanja la Mulungu landikhudza.
22 Mundilondola bwanji ngati Mulungu,
losakukwanirani thupi langa?
23 Ha! Akadalembedwa mau anga!
Ha! Akadalembedwa m’buku!
24 Akadawazokota pathanthwe chikhalire,
ndi chozokotera chachitsulo ndi kuthira ntovu!
25 Koma ndidziwa kuti Mombolo wanga ali ndi moyo,
nadzauka potsiriza pafumbi.
26 Ndipo khungu langa litaonongeka,
pamenepo wopanda thupi langa, ndidzapenya Mulungu,
27 amene ndidzampenya ndekha,
ndi maso anga adzamuona, si wina ai.
Imso zanga zatha m’kati mwanga.
28 Mukati, Tiyeni timlondole!
Popeza chifukwa cha mlandu chapezeka mwa ine;
29 muchite nalo mantha lupanga;
pakuti mkwiyo utenga zolakwa za lupanga,
kuti mudziwe pali chiweruzo.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/19-a97e6e764d67158b755f3690a23fa43c.mp3?version_id=1068—