Categories
YOBU

YOBU 22

Elifazi amtchulira Yobu zoipa zambiri, namuuza alape, Mulungu nadzamchitira chifundo

1 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,

2 Kodi munthu apindulira Mulungu?

Koma wanzeru angodzipindulira yekha.

3 Kodi Wamphamvuyonse akondwera nako

kuti iwe ndiwe wolungama?

Kapena kodi apindula nako kuti ukwaniritsa njira zako?

4 Kodi akudzudzula, nadza nawe kumlandu,

chifukwa cha kumuopa kwako?

5 Zoipa zako sizichuluka kodi?

Ndi mphulupulu zako sizikhala zosawerengeka kodi?

6 Pakuti wamtenga chikole kwa mbale wako wopanda chifukwa,

ndi kuvula ausiwa zovala zao.

7 Sunampatsa wolema madzi amwe,

ndi wanjala unammana chakudya.

8 Koma munthu mwini mphamvu, dziko ndi lake;

ndi munthu wovomerezeka, anakhala momwemo.

9 Unabweza akazi amasiye osawaninkha kanthu,

ndi manja a ana amasiye anathyoledwa.

10 Chifukwa chake misampha ikuzinga.

Ndi mantha akuvuta modzidzimutsa,

11 kapena mdima kuti ungaone,

ndi madzi aunyinji akumiza.

12 Kodi Mulungu sakhala m’mwamba m’tali?

Ndipo penyani kutalika kwake kwa nyenyezi, zili m’talitali.

13 Ndipo ukuti, Adziwa chiyani Mulungu?

Aweruza kodi mwa mdima wa bii?

14 Mitambo ndiyo chomphimba, kuti angaone;

ndipo amayenda pa thambo lakumwamba.

15 Udzasunga kodi njira yakale,

anaiponda anthu amphulupulu?

16 Amene anakwatulidwa isanafike nyengo yao,

chigumula chinakokolola kuzika kwao;

17 amene anati kwa Mulungu, Tichokereni;

ndipo, Angatichitire chiyani Wamphamvuyonse?

18 Angakhale Iye adadzaza nyumba zao ndi zabwino;

koma uphungu wa oipa unditalikira.

19 Olungama achiona nakondwera;

ndi osalakwa awaseka pwepwete,

20 ndi kuti, Zoonadi, otiukirawo alikhidwa,

ndi zowatsalira, moto unazipsereza.

21 Uzolowerane ndi Iye, nukhale ndi mtendere;

ukatero zokoma zidzakudzera.

22 Landira tsono chilamulo pakamwa pake,

nuwasunge maneno ake mumtima mwako.

23 Ukabweranso kwa Wamphamvuyonse, udzamanga bwino;

ukachotsera chosalungama kutali kwa mahema ako.

24 Ndipo utaye chuma chako kufumbi,

ndi golide wa ku Ofiri ku miyala ya kumitsinje.

25 Ndipo Wamphamvuyonse adzakhala chuma chako,

ndi ndalama zako zofunika.

26 Pakuti pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuyonse,

ndi kuweramutsa nkhope yako kwa Mulungu.

27 Udzampemphera ndipo adzakumvera;

nudzatsiriza zowinda zako.

28 Ukatsimikiza mtima kakuti, kadzakhazikikira iwe;

ndi kuunika kudzawala panjira zako.

29 Anthu akakugwetsa pansi, udzati, Adzandikweza;

ndipo adzapulumutsa wodzichepetsayo.

30 Adzamasula ngakhale wopalamula,

inde adzamasuka mwa kuyera kwa manja ako.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/22-0c8eaf0ad4df2bd7f5ecabd45970a9c9.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *