Yobu adzikaniza nanenetsa kuti ochimwa ambiri akhala osalangidwa. Ena ali ndi nzeru ndi chuma, koma opanda nzeru yeniyeni
1 Ndipo Yobu anaonjezanso mwambi wake, nati,
2 Pali Mulungu, amene anandichotsera zoyenera ine,
ndi Wamphamvuyonse, amene anawawitsa moyo wanga,
3 pakuti moyo wanga wonse ukali mwa ine,
ndi mpweya wa Mulungu m’mphuno mwanga;
4 milomo yanga siilankhula chosalungama,
ndi lilime langa silitchula zachinyengo.
5 Sindivomereza konse kuti muli olungama;
mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.
6 Ndiumirira chilungamo changa, osachileka;
chikhalire moyo ine, mtima wanga sunditonza.
7 Mdani wanga akhale ngati woipa,
ndi iye amene andiukira ngati wosalungama.
8 Pakuti chiyembekezo cha wonyoza Mulungu nchiyani pomlikhatu Mulungu,
pomchotsera moyo wake?
9 Kodi Mulungu adzamvera kufuula kwake, ikamdzera nsautso?
10 Kodi adzadzikondweretsa naye Wamphamvuyonse,
ndi kuitana kwa Mulungu nthawi zonse?
11 Ndidzakulangizani za dzanja la Mulungu;
chokhala ndi Wamphamvuyonse sindidzachibisa.
12 Taonani, inu nonse munachiona;
ndipo mugwidwa nazo zopanda pake chifukwa ninji?
13 Ili ndi gawo la munthu woipa kwa Mulungu,
ndi cholowa cha akupsinja anzao achilandira kwa Wamphamvuyonse.
14 Akachuluka ana ake, ndiko kuchulukira lupanga,
ndi ana ake sadzakhuta chakudya.
15 Akumtsalira iye adzaikidwa muimfa,
ndi akazi ake amasiye sadzalira maliro.
16 Chinkana akundika ndalama ngati fumbi,
ndi kukonzeratu zovala ngati dothi;
17 azikonzeretu, koma wolungama adzazivala,
ndi wosalakwa adzagawa ndalamazo.
18 Amanga nyumba yake ngati kangaude,
ndi ngati wolindira amanga dindiro.
19 Agona pansi ali wachuma, koma saikidwa;
potsegula maso ake, wafa chikomo.
20 Zoopsa zimgwera ngati madzi;
nkuntho umtenga usiku.
21 Mphepo ya kum’mawa imtenga, nachoka iye;
nimkankha achoke m’malo mwake.
22 Pakuti Mulungu adzamponyera zoopsa, osamleka;
kuthawa akadathawa m’dzanja lake.
23 Anthu adzamuombera manja,
nadzamuimbira mluzu achoke m’malo mwake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/27-bd63e4d17d63827b5beea54c88b61219.mp3?version_id=1068—