Categories
YOBU

YOBU 28

1 Koma kuli mtapo wasiliva,

ndi malo a golide amene amuyenga.

2 Chitsulo achitenga m’nthaka,

ndi mkuwa ausungunula kumwala.

3 Munthu athawitsa mdima,

nafunafuna mpaka malekezero onse,

miyala ya mdima wa bii ndi ya mthunzi wa imfa.

4 Aboola mgodi posiyana patali pokhala anthu;

aiwalika ndi phazi lopitapo;

apachikika kutali ndi anthu, nalendewalendewa.

5 Kunena za nthaka, kuchokera momwemo mumatuluka chakudya,

ndi m’munsi mwake musandulizika ngati ndi moto.

6 Miyala yake ndiyo malo a safiro,

ndipo ili nalo fumbi lagolide.

7 Njira imeneyi palibe chiombankhanga chiidziwa;

lingakhale diso la kabawi losapenyapo.

8 Nyama zodzikuza sizinapondapo,

ngakhale mkango waukali sunapitapo.

9 Munthu atambasulira dzanja lake kumwala;

agubuduza mapiri kuyambira kumizu.

10 Asema njira pakati pa matanthwe,

ndi diso lake liona chilichonse cha mtengo wake.

11 Atseka mitsinje ingadonthe;

natulutsira poyera chobisikachi.

12 Koma nzeru, idzapezeka kuti?

Ndi luntha, malo ake ali kuti?

13 Munthu sadziwa mtengo wake;

ndipo silipezeka m’dziko la amoyo.

14 Pozama pakuti, Mwa ine mulibe;

ndi nyanja ikuti, Kwa ine kulibe.

15 Silipezeka ndi golide,

sayesapo siliva mtengo wake.

16 Sailinganiza ndi golide wa Ofiri,

ndi sohamu wa mtengo wake wapatali kapena safiro.

17 Golide ndi krustalo sizilingana nayo;

ndi kusinthana kwake,

siisinthanika ndi zisambiro za golide woyengetsa.

18 Korali kapena ngale sizikumbukikapo.

Mtengo wake wa nzeru uposa wa korali wofiira.

19 Topazi wa Kusi sufanana nayo,

sailinganiza ndi golide wolongosoka.

20 Koma nzeru ifuma kuti?

Ndi luntha, pokhala pake pali kuti?

21 Popeza pabisikira maso a zamoyo zonse,

pabisikiranso mbalame za m’mlengalenga.

22 Chionongeko ndi Imfa zikuti,

Tamva mbiri yake m’makutu mwathu.

23 Mulungu ndiye azindikira njira yake,

ndiye adziwa pokhala pake.

24 Pakuti apenyerera malekezero a dziko lapansi,

naona pansi pa thambo ponse;

25 pamene anaikira mphepo muyeso wake,

nayesera madzi miyeso;

26 pakuchitira mvula lamulo,

ndi njira yoyendamo mphezi ya bingu;

27 pamenepo anaiona nzeru, naifotokozera;

anaikonza, naisanthula.

28 Koma kwa munthu anati,

Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru;

ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/28-e038ea55e9281f6c3929e8f7b1f4b24b.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *