1 Pa ichinso mtima wanga unjenjemera,
nusunthika m’malo mwake.
2 Mvetsetsani chibumo cha mau ake,
ndi kugunda kotuluka m’kamwa mwake.
3 Akumveketsa pansi pa thambo ponse,
nang’anipitsa mphezi yake ku malekezero a dziko lapansi.
4 Mau abuma kuitsata,
agunda ndi mau a ukulu wake,
ndipo sailetsa atamveka mau ake.
5 Mulungu agunda modabwitsa ndi mau ake,
achita zazikulu osazidziwa ife.
6 Pakuti anena kwa chipale chofewa, Ugwe padziko,
momwemonso kwa mvula,
ndi kwa mvumbi waukulu.
7 Atsekereza mokhomera chizindikiro dzanja la munthu aliyense,
kuti anthu onse anawalenga adziwe.
8 Pamenepo zilombo zilowa mobisalamo,
ndipo zikhala m’ngaka mwao.
9 M’chipinda mwake mutuluka kamvulumvulu,
ndi chisanu chifuma kumpoto.
10 Mwa kupuma kwake Mulungu apereka chipale,
ndi madzi achitando aundana.
11 Asenzetsanso mtambo wakuda bii madzi,
afunyulula mtambo wokhalamo mphezi yake;
12 ndipo utembenukatembenuka pakulangiza kwake,
kuti uchite zilizonse aulamulira,
pa nkhope ya dziko lokhalamo anthu;
13 ngati aufikitsira dziko lake kulidzudzula,
kapena kulichitira chifundo.
14 Tamverani ichi, Yobu.
Taimani, mulingirire zodabwitsa za Mulungu.
15 Kodi mudziwa umo Mulungu azilangizira zimenezi,
nawalitsa mphezi ya m’mtambo mwake?
16 Kodi mudziwa madendekeredwe ake a mitambo,
zodabwitsa za Iye wakudziwa mwangwiro?
17 Kodi mudziwa umo zovala zanu zifundira,
pamene dziko lili thuu chifukwa cha mwera?
18 Kodi muyala thambo pamodzi ndi Iye,
ndilo lolimba ngati kalirole woyengeka?
19 Mutilangize chimene tidzanena ndi Iye;
sitidziwa kulongosola mau athu chifukwa cha mdima.
20 Kodi munthu ayenera kumuuza kuti ndifuna kunena,
kapena kodi munthu adzakhumba kumezedwa?
21 Ndipo tsopano anthu sangathe kupenyerera kuunika
pakunyezimira kuthambo,
ndi mphepo yapita ndi kuuyeretsa.
22 Kuchokera kumpoto kudzera kuwala konyezimira,
Mulungu ali nao ukulu woopsa.
23 Kunena za Wamphamvuyonse, sitingamsanthule;
ndiye wa mphamvu yoposa;
koma mwa chiweruzo ndi chilungamo chochuluka samasautsa.
24 M’mwemo anthu amuopa,
Iye sasamalira aliyense wanzeru mumtima.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/37-f2fd93babd3776ddcbe1246e5ad4081f.mp3?version_id=1068—