1 Ndipo Yehova anabwereza kwa Yobu, nati,
2 Kodi wodzudzulayo atsutsane ndi Wamphamvuyonse?
Wochita makani ndi Mulungu ayankhe.
3 Pamenepo Yobu anayankha Yehova nati,
4 Taonani, ndakhululuka ine, ndidzakubwezerani mau otani?
Ndigwira pakamwa.
5 Ndalankhula kamodzi, koma sindidzayankha;
inde kawiri, koma sindionjezanso.
6 Ndipo Yehova anamyankha Yobu m’kamvulumvulu, nati,
7 Dzimangire m’chuuno tsono ngati mwamuna;
ndidzakufunsa, undidziwitse.
8 Chingakhale chiweruzo changa udzachithyola kodi?
Udzanditsutsa kuti ndili woipa kodi,
kuti ukhale wolungama ndiwe?
9 Kodi uli nalo dzanja ngati Ine Mulungu?
Kapena ukhoza kugunda ndi mau ngati Ine?
10 Udzikometsere tsono ndi ukulu ndi kukuzika,
nuvale ulemu ndi ulemerero.
11 Tsanulira mkwiyo wako wosefuka,
nupenyerere aliyense wodzikuza ndi kumchepetsa.
12 Upenyerere aliyense wodzikuza, numtsitse,
nupondereze oipa pomwe akhala.
13 Uwakwirire pamodzi m’fumbi,
uzimange nkhope zao pobisika.
14 Pamenepo inenso ndidzakuvomereza,
kuti dzanja lakolako lamanja likupulumutsa.
15 Tapenya tsono mvuu ndinaipanga pamodzi ndi iwe,
ikudya udzu ngati ng’ombe.
16 Tapenya tsono, mphamvu yake ili m’chuuno mwake,
ndi kulimbalimba kwake kuli m’mitsempha ya m’mimba yake.
17 Igwedeza mchira wake ngati mkungudza;
mitsempha ya ntchafu zake ipotana.
18 Mafupa ake akunga misiwe yamkuwa;
ziwalo zake zikunga zitsulo zamphumphu.
19 Iyo ndiyo chiyambi cha machitidwe a Mulungu;
wakuilenga anaininkha lupanga lake.
20 Pakuti mapiri aiphukitsira chakudya,
kumene zisewera nyama zonse zakuthengo.
21 Igona pansi patsinde pa mitengo yamthunzi,
pobisala pabango ndi pathawale.
22 Mitengo yamthunzi iiphimba ndi mthunzi wao,
misondodzi ya kumtsinje iizinga.
23 Taona madzi a mumtsinje akakula, siinjenjemera;
ilimbika mtima, ngakhale Yordani atupa mpaka pakamwa pake.
24 Ikakhala maso, munthu adzaigwira kodi?
Kapena kuboola m’mphuno mwake ili m’khwekhwe?
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/40-1e6529ccf0fa7095a692e8a602fb6a4d.mp3?version_id=1068—