Pemphero posautsidwa
Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto. Salimo la Davide.
1 Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa;
pondichepera mwandikulitsira malo.
Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.
2 Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti?
Mudzakonda zachabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti?
3 Koma dziwani kuti Yehova anadzipatulira yekha womkondayo,
adzamva Yehova m’mene ndimfuulira Iye.
4 Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe.
Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.
5 Iphani nsembe za chilungamo,
ndipo mumkhulupirire Yehova.
6 Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani?
Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.
7 Mwapatsa chimwemwe mumtima mwanga,
chakuposa chao m’nyengo yakuchuluka dzinthu zao ndi vinyo wao.
8 Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo;
chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/4-41ebdc08e25d9ab62ee6ed79d53b14ad.mp3?version_id=1068—