Matsoka a oipa, madalitso a olungama
Kwa Mkulu wa Nyimbo: aimbire zitoliro. Salimo la Davide.
1 Mverani mau anga, Yehova, Zindikirani kulingirira kwanga.
2 Tamvetsani mau a kufuula kwanga,
Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga;
pakuti kwa Inu ndimapemphera.
3 M’mawa, Yehova, mudzamva mau anga;
m’mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.
4 Pakuti Inu sindinu Mulungu wakukondwera nacho choipa
mphulupulu siikhala ndi Inu.
5 Opusa sadzakhazikika pamaso panu,
mudana nao onse akuchita zopanda pake.
6 Mudzaononga iwo akunena bodza;
munthu wokhetsa mwazi ndi wachinyengo,
Yehova anyansidwa naye.
7 Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu
ndidzalowa m’nyumba yanu;
ndidzagwada kuyang’ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.
8 Yehova, munditsogolere m’chilungamo chanu,
chifukwa cha akundizondawo;
mulungamitse njira yanu pamaso panga.
9 Pakuti m’kamwa mwao mulibe mau okhazikika;
m’kati mwao m’mosakaza;
m’mero mwao ndi manda apululu;
lilime lao asyasyalika nalo.
10 Muwayese otsutsika Mulungu;
agwe nao uphungu wao.
M’kuchuluka kwa zolakwa zao muwapirikitse;
pakuti anapikisana ndi Inu.
11 Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu,
afuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira;
nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu.
12 Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo;
mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/5-7ac8e9291abfdad07ec8a74c1b4764ae.mp3?version_id=1068—