Categories
MASALIMO

MASALIMO 32

Mwai wa munthu amene Mulungu wamkhululukira

Salimo la Davide. Chilangizo.

1 Wodala munthuyo wokhululukidwa tchimo lake;

wokwiriridwa choipa chake.

2 Wodala munthuyu Yehova samwerengera mphulupulu zake;

ndimo mumzimu mwake mulibe chinyengo.

3 Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba

ndi kubuula kwanga tsiku lonse.

4 Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine;

uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.

5 Ndinavomera choipa changa kwa Inu;

ndipo mphulupulu yanga sindinaibise.

Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga;

ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.

6 Chifukwa chake oyera mtima onse apemphere kwa Inu,

pa nthawi ya kupeza Inu;

indetu pakusefuka madzi aakulu

sadzamfikira iye.

7 Inu ndinu mobisalira mwanga;

m’nsautso mudzandisunga;

mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.

8 Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo;

ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.

9 Musakhale monga kavalo, kapena ngati bulu, wopanda nzeru;

zomangira zao ndizo cham’kamwa ndi chapamutu zakuwakokera,

pakuti ukapanda kutero sadzakuyandikiza.

10 Zisoni zambiri zigwera woipa;

koma chifundo chidzamzinga iye wakukhulupirira Yehova.

11 Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima;

ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/32-8b62cf41b1629155077301dc08c38e74.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *