Categories
MASALIMO

MASALIMO 36

Kuipitsitsa kwa anthu, kukometsetsa kwa Mulungu

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova.

1 Cholakwa cha woipayo chimati m’kati mwa mtima wanga,

palibe kuopa Mulungu pamaso pake.

2 Pakuti adzidyoletsa yekha m’kuona kwake,

kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho.

3 Mau a pakamwa pake ndiwo opanda pake ndi onyenga,

waleka kuzindikira ndi kuchita bwino.

4 Alingirira zopanda pake pakama pake;

adziika panjira posati pabwino;

choipa saipidwa nacho.

5 Yehova, m’mwamba muli chifundo chanu;

choonadi chanu chifikira kuthambo.

6 Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu;

maweruzo anu akunga chozama chachikulu,

Yehova, musunga munthu ndi nyama.

7 Ha! Chifundo chanu, Mulungu, nchokondedwadi!

Ndipo ana a anthu athawira kumthunzi wa mapiko anu.

8 Adzakhuta kwambiri ndi zonona za m’nyumba mwanu,

ndipo mudzawamwetsa mu mtsinje wa zokondweretsa zanu.

9 Pakuti chitsime cha moyo chili ndi Inu,

M’kuunika kwanu tidzaona kuunika.

10 Tanimphitsani chifundo chanu pa iwo akudziwa Inu;

ndi chilungamo chanu pa oongoka mtima.

11 Phazi la akudzikuza lisandifikire ine,

ndi dzanja la oipa lisandichotse.

12 Pomwepo padagwera ochita zopanda pake.

Anawalikha, ndipo sadzatha kuukanso.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/36-41066793019d717dbea4c3065b406512.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *