Categories
MASALIMO

MASALIMO 38

Davide awulula zoipa zake, apempha Mulungu amkhululukire namthandize

Salimo la Davide, lakukumbutsa.

1 Yehova, musandidzudzule ndi mkwiyo wanu,

ndipo musandilange moopsa m’mtima mwanu.

2 Pakuti mivi yanu yandilowa,

ndi dzanja lanu landigwera.

3 Mumnofu mwanga mulibe chamoyo chifukwa cha ukali wanu;

ndipo m’mafupa anga simuzizira, chifukwa cha cholakwa changa.

4 Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga;

ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera.

5 Mabala anga anunkha, adaola,

chifukwa cha kupusa kwanga.

6 Ndapindika, ndawerama kwakukulu;

ndimayenda woliralira tsiku lonse.

7 Pakuti m’chuuno mwanga mutentha kwambiri;

palibe pamoyo m’mnofu mwanga.

8 Ndafooka ine, ndipo ndachinjizidwa,

ndabangula chifukwa cha kumyuka mtima wanga.

9 Ambuye, chikhumbo changa chonse chili pamaso panu;

ndipo kubuula kwanga sikubisika kwa Inu.

10 Mtima wanga ugundagunda, mphamvu yanga yachoka,

ndipo kuunika kwa maso anga, ndi iko komwe kwandichokera.

11 Ondikonda ndi anzanga apewa mliri wanga;

ndipo anansi anga aima patali.

12 Ndipo anditchera misampha iwo akufuna moyo wanga;

ndipo iwo akuyesa kundichitira choipa alankhula zoononga,

nalingirira zonyenga tsiku lonse.

13 Koma ine, monga gonthi, sindimva;

ndipo monga munthu wosalankhula,

sinditsegula pakamwa panga.

14 Inde ndikunga munthu wosamva,

ndipo m’kamwa mwanga mulibe makani.

15 Pakuti ndikuyembekezani Inu, Yehova;

Inu mudzayankha, Ambuye Mulungu wanga.

16 Pakuti ndinati, Asakondwerere ine;

pakuterereka phazi langa, asadzikuze pa ine.

17 Ndafikana potsimphina,

ndipo chisoni changa chili pamaso panga chikhalire.

18 Pakuti ndidzafotokozera mphulupulu yanga;

nditenga nkhawa chifukwa cha tchimo langa.

19 Koma adani anga ali ndi moyo, nakhala ndi mphamvu,

ndipo akundida kopanda chifukwa achuluka.

20 Ndipo iwo akubwezera choipa pa chabwino

atsutsana nane, popeza nditsata chabwino.

21 Musanditaye, Yehova,

Mulungu wanga, musakhale kutali ndi ine.

22 Fulumirani kundithandiza,

Ambuye, chipulumutso changa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/38-7b3dae37b413a81d84a084883bd1d0e0.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *