1 Paulo, kapolo wa Mulungu, ndimtumwiwa YesuKhristu, monga mwa chikhulupiriro cha osankhika a Mulungu, ndi chizindikiritso cha choonadi chili monga mwa chipembedzo,
2 m’chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthawi zosayamba;
3 koma pa nyengo za Iye yekha anaonetsa mau ake muulalikiro, umene anandisungitsa ine, monga mwa lamulo la Mpulumutsi wathu Mulungu:
4 kwa Tito, mwana wanga weniweni monga mwa chikhulupiriro cha ife tonse: Chisomo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.
Asenzetsa Tito udindo wakusunga Mpingo wa ku Krete. Atsutsa aphunzitsi onyenga
5 Chifukwa cha ichi ndinakusiya iwe mu Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akulu m’midzi yonse, monga ndinakulamulira;
6 ngati wina ali wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nao ana okhulupirira, wosasakaza zake, kapena wosakana kumvera mau.
7 Pakuti woyang’anira ayenera kukhala wopanda chilema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati wachiwawa, wopanda ndeu, wosati wa chisiriro chonyansa;
8 komatu wokonda kuchereza alendo, wokonda zokoma, wodziweruza, wolungama, woyera mtima, wodziletsa;
9 wogwira mau okhulupirika monga mwa chiphunzitso, kuti akakhoze kuchenjeza m’chiphunzitso cholamitsa, ndi kutsutsa otsutsana naye.
10 Pakuti alipo ambiri osamvera mau, olankhula zopanda pake, ndi onyenga, makamaka iwo akumdulidwe,
11 amene ayenera kutsekedwa pakamwa; ndiwo amene apasula mabanja banja lonse, ndi kuphunzitsa zosayenera chifukwa cha chisiriro chonyansa.
12 Wina wa mwa iwo, ndiyemneneriwa iwo okha, anati, Akrete ndiwo amabodza masiku onse, zilombo zoipa, aumbombo, aulesi.
13 Umboni uwu uli woona. Mwa ichi uwadzudzule mokalipa, kuti akakhale olama m’chikhulupiriro,
14 osasamala nthano zachabe za Chiyuda, ndi malamulo a anthu opatuka kusiyana nacho choonadi.
15 Zonse ziyera kwa iwo amene ayera mtima; koma kwa iwo odetsedwa ndi osakhulupirira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zao ndi chikumbumtima chao.
16 Avomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zao amkana Iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/TIT/1-e0ea9c6fabc561b7d3999df629e672ce.mp3?version_id=1068—