Anthu a Mulungu akumbuke zithandizo zakale popempha chipulumutso m’tsoka lao
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Chilangizo cha kwa ana a Kora.
1 Mulungu, tidamva m’makutu mwathu, makolo athu anatisimbira,
za ntchitoyo mudaichita masiku ao, masiku akale.
2 Inu munapirikitsaamitundundi dzanja lanu,
koma iwowa munawaoka;
munasautsa mitundu ya anthu, ndipo munawaingitsa.
3 Pakuti sanalande dziko ndi lupanga lao,
ndipo mkono wao sunawapulumutse.
Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu,
ndi kuunika kwa nkhope yanu.
Popeza munakondwera nao,
4 Inu ndinu mfumu yanga, Mulungu;
lamulirani chipulumutso cha Yakobo.
5 Mwa Inu tidzakankhira pansi otsutsana nafe,
m’dzina lanu tidzapondereza akutiukira ife.
6 Pakuti uta wanga,
ndipo lupanga langa silingandipulumutse.
7 Koma Inu munatipulumutsa kwa iwo akutsutsana nafe,
ndipo akudana nafe, mudawachititsa manyazi.
8 Mwa Mulungu tidzitamanda tsiku lonse,
ndipo dzina lanu tidzaliyamika kosatha.
9 Koma mwatitaya, ndi kutinyazitsa;
ndipo simutuluka nao makamu a nkhondo athu.
10 Mutibwereretsa kuthawa otisautsa,
ndipo akudana nafe adzifunkhira okha.
11 Mwatipereka ngati nkhosa zoyenera kuzidya;
ndipo mwatibalalitsa mwa amitundu.
12 Mugulitsa anthu anu kwachabe,
ndipo mtengo wake simupindula nao.
13 Mutisandutsa chotonza kwa anzathu,
ndi choseketsa ndi cholalatitsa iwo akutizinga.
14 Mutiika tikhale onyozeka mwa amitundu,
ndi kuti anthu atipukusire mitu.
15 Tsiku lonse chimpepulo changa chikhala pamaso panga,
ndipo manyazi a pankhope panga andikuta.
16 Chifukwa cha mau a wotonza wochitira mwano;
chifukwa cha mdani ndi wobwezera chilango.
17 Zonsezi zatigwera; koma sitinakuiwalani,
ndipo sitinachite monyenga m’pangano lanu.
18 Mtima wathu sunabwerere m’mbuyo,
ndipo m’mayendedwe athu sitinapatuke m’njira yanu;
19 mungakhale munatithyola mokhala zilombo,
ndi kutiphimba nao mthunzi wa imfa.
20 Tikadaiwala dzina la Mulungu wathu,
ndi kutambasulira manja athu kwa mulungu wachilendo;
21 Mulungu sakadasanthula ichi kodi?
Pakuti adziwa zinsinsi za mtima.
22 Koma, chifukwa cha Inu, tiphedwa tsiku lonse;
tiyesedwa ngati nkhosa zakuzipha.
23 Galamukani, mugoneranji, Ambuye?
Ukani, musatitaye chitayire.
24 Mubisiranji nkhope yanu,
ndi kuiwala kuzunzika ndi kupsinjika kwathu?
25 Pakuti moyo wathu waweramira kufumbi,
pamimba pathu pakangamira dziko lapansi.
26 Ukani, tithandizeni,
tiomboleni mwa chifundo chanu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/44-de9af6db6f1f40d0e02f99000a4b2758.mp3?version_id=1068—