Ukoma ndi ulemerero wa Ziyoni
Nyimbo. Salimo la ana a Kora.
1 Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi,
m’mzinda wa Mulungu wathu, m’phiri lake loyera.
2 Phiri laZiyoni, chikhalidwe chake nchokoma
kumbali zake za kumpoto,
ndilo chimwemwe cha dziko lonse lapansi,
mzinda wa mfumu yaikulu.
3 Mulungu adziwika m’zinyumba zake ngati msanje.
4 Pakuti, taonani, mafumuwo anasonkhana,
anapitira pamodzi.
5 Anapenya mudziwo, ndipo pamenepo anadabwa;
anaopsedwa, nathawako.
6 Pomwepo anagwidwa nako kunthunthumira;
anamva chowawa, ngati wam’chikuta.
7 Muswa zombo za ku Tarisisi ndi mphepo ya kum’mawa.
8 Monga tidamva, momwemo tidapenya
m’mzinda wa Yehova wa makamu, m’mzinda wa Mulungu wathu,
Mulungu adzaukhazikitsa kunthawi yamuyaya.
9 Tidalingalira zachifundo chanu, Mulungu,
m’kati mwa Kachisi wanu.
10 Monga dzina lanu, Mulungu,
momwemo lemekezo lanu ku malekezero a dziko lapansi;
m’dzanja lamanja lanu mudzala chilungamo.
11 Likondwere phiri la Ziyoni,
asekere ana aakazi a Yuda,
chifukwa cha maweruzo anu.
12 Zungulirani Ziyoni, ndipo muuzinge,
werengani nsanja zake.
13 Penyetsetsani malinga ake,
yesetsani zinyumba zake;
kuti mukaziwerengere mibadwo ikudza m’mbuyo.
14 Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu
kunthawi za nthawi,
adzatitsogolera kufikira imfa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/48-ba5befffea5b0683b72b66ebb5cb961c.mp3?version_id=1068—