Categories
MASALIMO

MASALIMO 63

Mtima woliralira kuyanjana ndi Mulungu

Salimo la Davide; muja anakhala m’chipululu cha Yuda.

1 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga;

ndidzakufunani m’matanda kucha.

Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu,

thupi langa lilirira Inu,

m’dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.

2 Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu,

monga ndinakuonani m’malo oyera.

3 Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake;

milomo yanga idzakulemekezani.

4 Potero ndidzakuyamikani m’moyo mwanga;

ndidzakweza manja anga m’dzina lanu.

5 Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona;

ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani

ndi milomo yakufuula mokondwera.

6 Pokumbukira Inu pa kama wanga,

ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku.

7 Pakuti munakhala mthandizi wanga;

ndipo ndidzafuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.

8 Moyo wanga uumirira Inu.

Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.

9 Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge,

adzalowa m’munsi mwake mwa dziko.

10 Adzawapereka kumphamvu ya lupanga;

iwo adzakhala gawo la ankhandwe.

11 Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;

yense wakulumbirira iye adzatamandira;

pakuti pakamwa pa iwo onena bodza padzatsekedwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/63-dd5022b579c322c447c9f170e2fa695e.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *