Categories
MASALIMO

MASALIMO 64

Davide apempha Mulungu amtchinjirize pa omlalira

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Imvani Mulungu, mau anga, m’kudandaula kwanga;

sungani moyo wanga angandiopse mdani.

2 Ndibiseni pa upo wachinsinsi wa ochita zoipa;

pa phokoso la ochita zopanda pake.

3 Amene anola lilime lao ngati lupanga,

napiringidza mivi yao, ndiyo mau akuwawitsa;

4 kuponyera wangwiro mobisika:

Amponyera modzidzimutsa, osaopa.

5 Alimbikitsana m’chinthu choipa;

apangana za kutchera misampha mobisika;

akuti, Adzaiona ndani?

6 Afunafuna zosalungama; kusanthula, asanthuladi mpaka kutha;

chingakhale cha m’kati mwake mwa munthu, ndi mtima wozama.

7 Koma Mulungu adzawaponyera muvi;

adzalaswa modzidzimutsa.

8 Adzawakhumudwitsa, lilime lao lidzawatsutsa;

onse akuwaona adzawathawa.

9 Ndipo anthu onse adzachita mantha;

nadzabukitsa chochita Mulungu,

nadzasamalira ntchito yake.

10 Wolungama adzakondwera mwa Yehova,

nadzakhulupirira Iye;

ndipo oongoka mtima onse adzalemekeza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/64-f8cb3fc909cb65eb3e048846840dd693.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *