Davide alemekeza Mulungu pa madalitso ochuluka
Kwa Mkulu wa Nyimbo: Salimo la Davide. Nyimbo.
1 MuZiyoniakulemekezani Inu mwachete, Mulungu,
adzakuchitirani Inu chowindachi.
2 Wakumva pemphero Inu,
zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.
3 Mphulupulu zinandipambana;
koma mudzafafaniza zolakwa zathu.
4 Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa,
akhale m’mabwalo anu.
Tidzakhuta nazo zokoma za m’nyumba yanu,
za m’malo oyera a Kachisi wanu.
5 Mudzatiyankha nazo zoopsa m’chilungamo,
Mulungu wa chipulumutso chathu;
ndinu chikhulupiriko cha malekezero onse a dziko lapansi,
ndi cha iwo okhala kutali kunyanja.
6 Ndinu amene mukhazikitsa mapiri ndi mphamvu yanu;
pozingidwa nacho chilimbiko.
7 Amene atontholetsa kukuntha kwa nyanja,
kukuntha kwa mafunde ake,
ndi phokoso la mitundu ya anthu.
8 Ndipo iwo akukhala kumalekezero adzachita mantha
chifukwa cha zizindikiro zanu;
mukondweretsa apo patulukira dzuwa, ndi apo lilowera.
9 Mucheza nalo dziko lapansi, mulithirira,
mulilemeretsa kwambiri;
mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi,
muwameretsera tirigu m’mene munakonzera nthaka.
10 Mukhutitsa nthaka yake yolima;
mufafaniza nthumbira zake;
muiolowetsa ndi mvumbi;
mudalitsa mmera wake.
11 Muveka chakachi ndi ukoma wanu;
ndipo mabande anu akukha zakucha.
12 Akukha pa mabusa a m’chipululu;
ndipo mapiri azingika nacho chimwemwe.
13 Podyetsa mpodzaza ndi zoweta;
ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu;
zifuula mokondwera, inde ziimbira.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/65-b7355099f446294b6dd7e354ffe4751b.mp3?version_id=1068—