Davide adandaulira kwa Mulungu chifukwa cha zowawa azimva
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Pa Syosyanimu. Salimo la Davide.
1 Ndipulumutseni Mulungu;
pakuti madzi afikira moyo wanga.
2 Ndamira m’thope lozama, lopanda poponderapo;
ndalowa m’madzi ozama, ndipo chigumula chandimiza.
3 Ndalema ndi kufuula kwanga; kum’mero kwauma gwaa!
M’maso mwanga mwada poyembekeza Mulungu wanga.
4 Ondida kopanda chifukwa achuluka
koposa tsitsi la pamutu panga;
ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu.
Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine.
5 Mulungu, mudziwa kupusa kwanga;
ndipo kutsutsika kwanga sikubisikira Inu.
6 Iwo akuyembekeza Inu, Ambuye, Yehova wa makamu,
asachite manyazi chifukwa cha ine,
iwo ofuna Inu, Mulungu wa Israele,
asapepulidwe chifukwa cha ine.
7 Pakuti ndalola chotonza chifukwa cha Inu,
chimpepulo chakuta nkhope yanga.
8 Abale anga andiyesa mlendo,
ndi ana a mai wanga andiyesa wa mtundu wina.
9 Pakuti changu cha pa nyumba yanu chandidya;
ndi zotonza za iwo otonza Inu zandigwera ine.
10 Ndipo ndinalira pa kusala kwa moyo wanga,
koma uku kunandikhalira chotonza.
11 Ndipo chovala changa ndinayesa chiguduli,
koma amandiphera mwambi.
12 Okhala pachipata akamba za ine;
ndipo oledzera andiimba.
13 Koma ine, pemphero langa lili kwa Inu,
Yehova, m’nyengo yolandirika;
Mulungu, mwa chifundo chanu chachikulu,
mundivomereze ndi choonadi cha chipulumutso chanu.
14 Mundilanditse kuthope, ndisamiremo,
ndilanditseni kwa iwo akundida, ndi kwa madzi ozama.
15 Chigumula chisandifotsere,
ndipo chakuya chisandimize;
ndipo asanditsekere pakamwa pake pa dzenje.
16 Mundiyankhe Yehova; pakuti chifundo chanu nchokoma;
munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu.
17 Ndipo musabisire nkhope yanu mtumiki wanu;
pakuti ndisautsika ine; mundiyankhe msanga.
18 Yandikizani moyo wanga, ndi kuuombola;
ndipulumutseni chifukwa cha adani anga.
19 Mudziwa chotonza changa, ndi manyazi anga,
ndi chimpepulo changa.
Akundisautsa ali pamaso panu.
20 Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine;
ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe;
ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.
21 Ndipo anandipatsa ndulu ikhale chakudya changa;
nandimwetsa vinyo wosasa pomva ludzu ine.
22 Gome lao likhale msampha pamaso pao;
pokhala ndi mtendere iwo, likhale khwekhwe.
23 M’maso mwao mude, kuti asapenye;
ndipo munjenjemeretse m’chuuno mwao kosalekeza.
24 Muwatsanulire mkwiyo wanu,
ndipo moto wa ukali wanu uwagwere.
25 Pokhala pao pakhale bwinja;
m’mahema mwao musakhale munthu.
26 Pakuti alondola amene Inu munampanda;
ndipo akambirana za zowawa zao za iwo amene munawalasa.
27 Onjezani mphulupulu pa mphulupulu zao;
ndipo asafikire chilungamo chanu.
28 Afafanizidwe m’buku lamoyo,
ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.
29 Koma ine ndine wozunzika ndi womva zowawa;
chipulumutso chanu, Mulungu, chindikweze pamsanje.
30 Ndidzalemekeza dzina la Mulungu ndi kuliimbira,
ndipo ndidzambukitsa ndi kumyamika.
31 Ndipo chidzakomera Yehova koposa ng’ombe,
inde mphongo za nyanga ndi ziboda.
32 Ofatsa anachiona, nakondwera,
ndipo inu, ofuna Mulungu, mtima wanu ukhale ndi moyo.
33 Pakuti Yehova amvera aumphawi,
ndipo sapeputsa am’ndende ake.
34 Zakumwamba ndi dziko lapansi zimlemekeze,
nyanja ndi zonse zoyenda m’mwemo.
35 Pakuti Mulungu adzapulumutsaZiyoni,
nadzamanga mizinda ya Yuda;
ndipo iwo adzakhala komweko, likhale laolao.
36 Ndipo mbumba ya atumiki ake idzalilandira;
ndipo iwo akukonda dzina lake adzakhala m’mwemo.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/69-f68152a569022f718108a6f7b543097b.mp3?version_id=1068—