Za ufumu wa Mfumu yokoma
Salimo la Solomoni.
1 Patsani mfumu maweruzo anu, Mulungu,
ndi mwana wa mfumu chilungamo chanu.
2 Potero adzanenera anthu anu mlandu ndi m’chilungamo,
ndi ozunzika anu ndi m’chiweruzo.
3 Mapiri adzatengera anthu mtendere,
timapiri tomwe, m’chilungamo.
4 Adzaweruza ozunzika a mwa anthu,
adzapulumutsa ana aumphawi,
nadzaphwanya wosautsa.
5 Adzakuopani momwe likhalira dzuwa ndi mwezi,
kufikira mibadwomibadwo.
6 Adzanga mvula yakugwa pa udzu wosenga,
monga mvula yothirira dziko.
7 Masiku ake wolungama adzakhazikika;
ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi.
8 Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja,
ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi.
9 Okhala m’chipululu adzagwadira pamaso pake;
ndi adani ake adzaluma nthaka.
10 Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka;
mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso.
11 Inde mafumu onse adzamgwadira iye,
amitunduonse adzamtumikira.
12 Pakuti adzapulumutsa waumphawi wofuulayo;
ndi wozunzika amene alibe mthandizi.
13 Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi,
nadzapulumutsa moyo wa aumphawi.
14 Adzaombola moyo wao ku chinyengo ndi chiwawa;
ndipo mwazi wao udzakhala wa mtengo pamaso pake.
15 Ndipo iye adzakhala ndi moyo;
ndipo adzampatsa golide wa ku Sheba;
nadzampempherera kosalekeza;
adzamlemekeza tsiku lonse.
16 M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka
pamwamba pa mapiri;
zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebanoni,
ndipo iwo a m’mizinda adzaphuka ngati msipu wapansi.
17 Dzina lake lidzakhala kosatha,
momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu.
Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye;
amitundu onse adzamutcha wodala.
18 Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele,
amene achita zodabwitsa yekhayo.
19 Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha;
ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wake.
Amen, ndi Amen.
20 Mapemphero a Davide mwana wa Yese atha.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/72-afe1e9589ee32599b3e095cbb851cd4d.mp3?version_id=1068—