Mulungu woweruza asiyanitsa pakati pa odzikuza ndi olungama
Kwa Mkulu wa Nyimbo: Altasyeti. Salimo la Asafu. Nyimbo.
1 Tikuyamikani Inu, Mulungu;
tiyamika, pakuti dzina lanu lili pafupi;
afotokozera zodabwitsa zanu.
2 Pakuona nyengo yake ndidzaweruza molunjika.
3 Lasungunuka dziko lapansi, ndi onse okhalamo;
ndinachirika mizati yake.
4 Ndinati kwa odzitamandira,
musamachita zodzitamandira;
ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga;
5 musamakwezetsa nyanga yanu;
musamalankhula ndi khosi louma.
6 Pakuti kukuzaku sikuchokera kum’mawa,
kapena kumadzulo, kapena kuchipululu.
7 Pakuti Mulungu ndiye woweruza;
achepsa wina, nakuza wina.
8 Pakuti m’dzanja la Yehova muli chikho;
ndi vinyo wake achita thovu;
chidzala ndi zosakanizira, ndipo atsanulako.
Indedi, oipa onse a padziko lapansi adzamwa
nadzagugudiza nsenga zake.
9 Koma ine ndidzalalikira kosalekeza,
ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wa Yakobo.
10 Ndipo ndidzatseteka nyanga zonse za oipa;
koma nyanga za wolungama zidzakwezeka.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/75-52b7b03dd59f18d15cd25d480b6410d9.mp3?version_id=1068—