Mulungu atonza Aisraele pa kusamvera kwao
Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Gititi. Salimo la Asafu.
1 Imbitsirani Mulungu ndiye mphamvu yathu;
fuulirani kwa Mulungu wa Yakobo.
2 Utsani salimo, bwera nakoni kalingaka,
zeze wokondwetsa pamodzi ndi chisakasa.
3 Ombani lipenga, pokhala mwezi,
utakula mwezi, tsiku la phwando lathu.
4 Pakuti ichi ndi cholemba cha kwa Israele,
chiweruzo cha Mulungu wa Yakobo.
5 Anachiika chikhale mboni kwa Yosefe,
pakutuluka iye kudziko la Ejipito.
Komwe ndinamva chinenedwe chosadziwa ine.
6 Ndinamchotsera katundu paphewa pake,
manja ake anamasuka ku chotengera.
7 Unaitana posautsika, ndipo ndinakulanditsa;
ndinakuvomereza mobisalika m’bingu;
ndinakuyesa kumadzi a Meriba.
8 Tamvani, anthu anga, ndidzakuchitirani mboni;
Israele, ukadzandimvera!
9 Kwanu kusakhale mulungu wofuma kwina;
nusagwadire mulungu wachilendo.
10 Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakukweza
kukuchotsa kudziko la Ejipito;
yasamitsa pakamwa pako ndipo ndidzalidzaza.
11 Koma anthu anga sanamvere mau anga;
ndipo Israele sanandivomere.
12 Potero ndinawaperekera kuuma mtima kwao,
ayende monga mwa uphungu waowao.
13 Ha! Akadandimvera anthu anga,
akadayenda m’njira zanga Israele!
14 Ndikadagonjetsa adani ao msanga,
ndikadabweza dzanja langa pa owasautsa.
15 Akumuda Yehova akadamgonjera mungakhale monyenga,
koma nyengo yao ikadakhala yosatha.
16 Akadawadyetsa naye tirigu wokometsetsa,
ndikadakukhutitsanso ndi uchi wa m’thanthwe.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/81-7a6d9c36607a2edf7841f2afaaa781b5.mp3?version_id=1068—