Categories
MASALIMO

MASALIMO 89

Pangano la Mulungu ndi Davide Mulungu adzapulumutsa anthu ake

Chilangizo cha Etani Mwezara.

1 Ndidzaimbira zachifundo za Yehova nthawi yonse,

pakamwa panga ndidzadziwitsira chikhulupiriko chanu

ku mibadwomibadwo.

2 Pakuti ndinati, Chifundo adzachimanga kosaleka;

mudzakhazika chikhulupiriko chanu mu Mwamba mwenimweni.

3 Ndinachita chipangano ndi wosankhika wanga,

ndinalumbirira Davide mtumiki wanga.

4 Ndidzakhazika mbeu yako kunthawi yonse,

ndipo ndidzamanga mpando wachifumu wako ku mibadwomibadwo.

5 Ndipo kumwamba kudzalemekeza zodabwitsa zanu, Yehova;

chikhulupiriko chanunso mu msonkhano wa oyera mtima.

6 Pakuti kuli yani kuthambo timlinganize ndi Yehova?

Afanana ndi Yehova ndani mwa ana a amphamvu?

7 Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri mu upo wa oyera mtima,

ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.

8 Yehova, Mulungu wa makamu, wamphamvu ndani wonga Inu, Yehova?

Ndipo chikhulupiriko chanu chikuzingani.

9 Inu ndinu wakuchita ufumu pa kudzikuza kwa nyanja;

pakuuka mafunde ake muwachititsa bata.

10 Mudathyola Rahabu, monga munthu wophedwa;

munabalalitsa adani anu ndi mkono wa mphamvu yanu.

11 Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi lomwe ndi lanu;

munakhazika dziko lokhalamo anthu ndi kudzala kwake.

12 Munalenga kumpoto ndi kumwera;

Tabori ndi Heremoni afuula mokondwera m’dzina lanu.

13 Muli nao mkono wanu wolimba;

m’dzanja mwanu muli mphamvu, dzanja lamanja lanu nlokwezeka.

14 Chilungamo ndi chiweruzo ndiwo maziko a mpando wanu wachifumu;

chifundo ndi choonadi zitsogolera pankhope panu.

15 Odala anthu odziwa liu la lipenga;

ayenda m’kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.

16 Akondwera m’dzina lanu tsiku lonse;

ndipo akwezeka m’chilungamo chanu.

17 Popeza Inu ndinu ulemerero wa mphamvu yao;

ndipo potivomereza Inu nyanga yathu idzakwezeka.

18 Pakuti chikopa chathu chifuma kwa Yehova;

ndi mfumu yathu kwa Woyera wa Israele.

19 Pamenepo munalankhula m’masomphenya ndi okondedwa anu,

ndipo mudati, Ndasenza thandizo pa chiphona;

ndakweza wina wosankhika mwa anthu.

20 Ndapeza Davide mtumiki wanga;

ndamdzoza mafuta anga oyera.

21 Amene dzanja langa lidzakhazikika naye;

inde mkono wanga udzalimbitsa.

22 Mdani sadzamuumira mtima;

ndi mwana wa chisalungamo sadzamzunza.

23 Ndipo ndidzaphwanya omsautsa pamaso pake;

ndidzapandanso odana naye.

24 Koma chikhulupiriko changa ndi chifundo changa

zidzakhala naye;

ndipo nyanga yake idzakwezeka m’dzina langa.

25 Ndipo ndidzaika dzanja lake panyanja,

ndi dzanja lamanja lake pamitsinje.

26 Iye adzanditchula, ndi kuti, Inu ndinu Atate wanga,

Mulungu wanga, ndi thanthwe la chipulumutso changa.

27 Inde ndidzamuyesa mwana wanga woyamba,

womveka wa mafumu a padziko lapansi.

28 Ndidzamsungira chifundo changa kunthawi yonse,

ndipo chipangano changa chidzalimbika pa iye.

29 Ndidzakhalitsanso mbeu yake chikhalire,

ndi mpando wachifumu wake ngati masiku a m’mwamba.

30 Ana ake akataya chilamulo changa,

osayenda m’maweruzo anga,

31 nakaipsa malembo anga;

osasunga malamulo anga.

32 Pamenepo ndidzazonda zolakwa zao ndi ndodo,

ndi mphulupulu zao ndi mikwingwirima.

33 Koma sindidzamchotsera chifundo changa chonse,

ndi chikhulupiriko changa sichidzamsowa.

34 Sindidzaipsa chipangano changa,

kapena kusintha mau otuluka m’milomo yanga.

35 Ndinalumbira kamodzi m’chiyero changa;

sindidzanamizira Davide.

36 Mbeu yake idzakhala kunthawi yonse,

ndi mpando wachifumu wake ngati dzuwa pamaso panga.

37 Udzakhazikika ngati mwezi kunthawi yonse,

ndi ngati mboni yokhulupirika kuthambo.

38 Koma Inu munamtaya, nimunamkaniza,

munakwiya naye wodzozedwa wanu.

39 Munakaniza chipangano cha mtumiki wanu;

munaipsa korona wake ndi kumponya pansi.

40 Munapasula makoma ake onse;

munagumula malinga ake.

41 Onse opita panjirapa amfunkhira,

akhala chotonza cha anansi ake.

42 Munakweza dzanja lamanja la iwo omsautsa;

munakondweretsa adani ake onse.

43 Munapinditsa kukamwa kwake kwa lupanga lake,

osamuimika kunkhondo.

44 Munaleketsa kuwala kwake,

ndipo munagwetsa pansi mpando wachifumu wake.

45 Munafupikitsa masiku a mnyamata wake;

munamkuta nao manyazi.

46 Mudzabisala kosatha kufikira liti, Yehova;

ndi kuzaza kwanu kudzatentha ngati moto kufikira liti?

47 Kumbukirani kuti nthawi yanga njapafupi;

munalengeranji ana onse a anthu kwachabe?

48 Munthu ndani amene adzakhalabe ndi moyo, osaona imfa?

Amene adzapulumutsa moyo wake kumphamvu ya manda?

49 Chilikuti chifundo chanu chakale, Ambuye,

munachilumbirira Davide pa chikhulupiriko chanu?

50 Kumbukirani, Ambuye, chotonzera atumiki anu;

ndichisenza m’chifuwa mwanga

chochokera kumitundu yonse yaikulu ya anthu.

51 Chimene adani anu, Yehova, atonza nacho;

chimene atonzera nacho mayendedwe a wodzozedwa wanu.

52 Wodalitsika Yehova kunthawi yonse.

Amen ndi Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/89-440e7f8cad219e8890e8f4ad568878c7.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *