Categories
MASALIMO

MASALIMO 92

Anthu onse ayamike Mulungu chifukwa cha ntchito zake, chilungamo chake, ndi chifundo chake

Salimo, Nyimbo ya pa Sabata.

1 Nkokoma kuyamika Yehova,

ndi kuimbira nyimbo dzina lanu, Wam’mwambamwamba Inu.

2 Kuonetsera chifundo chanu mamawa,

ndi chikhulupiriko chanu usiku uliwonse.

3 Pa choimbira cha zingwe khumi ndi pachisakasa;

pazeze ndi kulira kwake.

4 Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kuchita kwanu,

ndidzafuula mokondwera pa ntchito ya manja anu.

5 Ha! Ntchito zanu nzazikulu, Yehova,

zolingalira zanu nzozama ndithu.

6 Munthu wopulukira sachidziwa;

ndi munthu wopusa sachizindikira ichi;

7 chakuti pophuka oipa ngati msipu,

ndi popindula ochita zopanda pake;

chitero kuti adzaonongeke kosatha.

8 Koma Inu, Yehova, muli m’mwamba kunthawi yonse.

9 Pakuti, taonani, adani anu, Yehova,

pakuti, taonani, adani anu adzatayika;

ochita zopanda pake onse adzamwazika.

10 Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati;

anandidzoza mafuta atsopano.

11 Diso langa lapenya chokhumba ine pa iwo ondilalira,

m’makutu mwanga ndamva chokhumba ine

pa iwo akuchita zoipa akundiukira.

12 Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa;

adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni.

13 Iwo ookedwa m’nyumba ya Yehova,

adzaphuka m’mabwalo a Mulungu wathu.

14 Atakalamba adzapatsanso zipatso;

adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri,

15 kulalikira kuti Yehova ngwolunjika;

Iye ndiye thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/92-932cff6c0bcd754f622cfa753d8f06fc.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *