Ulemerero wa ufumu wa Mulungu
1 Yehova achita ufumu; dziko lapansi likondwere;
zisumbu zambiri zikondwerere.
2 Pomzinga pali mitambo ndi mdima;
chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa
mpando wake wachifumu.
3 Moto umtsogolera,
nupsereza otsutsana naye pozungulirapo.
4 Mphezi zake zinaunikira dziko lokhalamo anthu;
dziko lapansi linaona nilinagwedezeka.
5 Mapiri anasungunuka ngati sera pamaso pa Yehova,
pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.
6 Kumwamba kulalikira chilungamo chake,
ndipo mitundu yonse ya anthu ipenya ulemerero wake.
7 Onse akutumikira fano losema,
akudzitamandira nao mafano, achite manyazi:
Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.
8 Ziyonianamva nakondwera,
nasekerera ana aakazi a Yuda;
chifukwa cha maweruzo anu, Yehova.
9 Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi,
ndinu wokwezeka kwakukulu pamwamba pa milungu ina yonse.
10 Inu okonda Yehova, danani nacho choipa:
Iye asunga moyo wa okondedwa ake;
awalanditsa m’manja mwa oipa.
11 Kuunika kufesekera wolungama,
ndi chikondwerero oongoka mtima.
12 Kondwerani mwa Yehova, olungama inu;
ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/97-6c65878c73f9e757113cb19d347e9fb8.mp3?version_id=1068—