Alemekeze Mulungu pa chifundo ndi choonadi chao
Salimo.
1 Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano;
popeza anachita zodabwitsa:
Dzanja lake lamanja, mkono wake woyera,
zinamchitira chipulumutso.
2 Yehova anawadziwitsira chipulumutso chake;
anaonetsera chilungamo chake pamaso pa amitundu.
3 Anakumbukira chifundo chake ndi chikhulupiriko chake
kunyumba ya Israele;
malekezero onse a dziko lapansi
anaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
4 Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi;
kuwitsani ndi kufuulira mokondwera;
inde, imbirani zomlemekeza.
5 Muimbireni Yehova zomlemekeza ndi zeze;
ndi zeze ndi mau a salimo.
6 Fuulani pamaso pa Mfumu Yehova,
ndi mbetete ndi liu la lipenga.
7 Nyanja ifuule ndi kudzala kwake;
dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhalamo;
8 mitsinje iombe m’manja;
mapiri afuule pamodzi mokondwera.
9 Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi;
adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo,
ndipo mitundu ya anthu molunjika.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/98-ac8f04ab9533726087f9e969fcb70cf5.mp3?version_id=1068—