Mulungu wamkulu wachifundo alemekezedwe
1 Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere;
Iye akhala pakati paakerubi; dziko lapansi ligwedezeke.
2 Yehova ndiye wamkulu muZiyoni;
ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.
3 Alemekeze dzina lanu lalikulu ndi loopsa.
Ili ndilo loyera.
4 Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda chiweruzo;
Inu mukhazikitsa zolunjika,
muchita chiweruzo ndi chilungamo mu Yakobo.
5 Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,
ndipo gwadirani poponderapo mapazi ake:
Iye ndiye Woyera.
6 Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni,
ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake;
anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.
7 Iye analankhula nao mu mtambo woti njo:
Iwo anasunga mboni zake ndi malembawa anawapatsa.
8 Munawayankha, Yehova Mulungu wathu:
munawakhalira Mulungu wakuwakhululukira,
mungakhale munabwezera chilango pa zochita zao.
9 Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,
ndipo gwadirani paphiri lake loyera;
pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/99-77e66ae4cdf6bfda694f115ffc645d1e.mp3?version_id=1068—