Davide aimbira Mulungu womgonjetsera adani
Nyimbo. Salimo la Davide.
1 Wakhazikika mtima wanga, Mulungu;
ndidzaimba, inde ndidzaimba zolemekeza, ndiko ulemerero wanga.
2 Galamukani, chisakasa ndi zeze;
ndidzauka ndekha mamawa.
3 Ndidzakuyamikani mwa mitundu ya anthu, Yehova:
ndipo ndidzaimba zakukulemekezani mwa anthu.
4 Pakuti chifundo chanu nchachikulu kupitirira kumwamba,
ndi choonadi chanu kufikira mitambo.
5 Kwezekani pamwamba pa thambo, Mulungu;
ndi ulemerero wanu pamwamba padziko lonse lapansi,
6 kuti okondedwa anu alanditsidwe,
pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja ndipo mutivomereze.
7 Mulungu analankhula m’chiyero chake; ndidzakondwerera:
ndidzagawa Sekemu; ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti.
8 Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanga;
ndi Efuremu ndiye mphamvu ya mutu wanga;
Yuda ndiye wolamulira wanga.
9 Mowabu ndiye mkhate wanga;
pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga;
ndidzafuulira Filistiya.
10 Adzandifikitsa ndani m’mzinda wa m’linga?
Adzanditsogolera ndani ku Edomu?
11 Si ndinu Mulungu, amene mwatitaya
osatuluka nao magulu athu?
12 Tithandizeni mumsauko;
pakuti chipulumutso cha munthu ndi chabe.
13 Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima:
Ndipo Iye adzapondereza otisautsa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/108-b23f6266034aa4eada30b38fe6a206bb.mp3?version_id=1068—