Davide apempha Mulungu alange oipa, amlanditse m’manja mwao
Kwa Mkulu wa Nyimbo: Salimo la Davide.
1 Mulungu wa chilemekezo changa, musakhale chete;
2 pakuti pakamwa pa woipa ndi pakamwa pa chinyengo pananditsegukira;
anandilankhulira ndi m’kamwa mwa bodza.
3 Ndipo anandizinga ndi mau a udani,
nalimbana nane kopanda chifukwa.
4 M’malo mwa chikondi changa andibwezera udani;
koma ine, kupemphera ndiko.
5 Ndipo anandisenza choipa m’malo mwa chokoma,
ndi udani m’malo mwa chikondi changa.
6 Muike munthu woipa akhale mkulu wake;
ndi mdani aime padzanja lamanja lake.
7 Ponenedwa mlandu wake atuluke wotsutsika;
ndi pemphero lake likhale ngati kuchimwa.
8 Masiku ake akhale owerengeka;
wina alandire udindo wake.
9 Ana ake akhale amasiye,
ndi mkazi wake wamasiye.
10 Ana ake akhale amchirakuyenda ndi opemphapempha;
afunefune zosowa zao kuchokera m’mabwinja mwao.
11 Wokongoletsa agwire zonse ali nazo;
ndi alendo alande za ntchito yake.
12 Pasakhale munthu wakumchitira chifundo;
kapena kuchitira chokoma ana ake amasiye.
13 Zidzukulu zake zidulidwe;
dzina lao lifafanizidwe mu mbadwo ukudza.
14 Mphulupulu za makolo ake zikumbukike ndi Yehova;
ndi tchimo la mai wake lisafafanizidwe.
15 Zikhale pamaso pa Yehova chikhalire,
kuti adule chikumbukiro chao kuchichotsera kudziko lapansi.
16 Chifukwa kuti sanakumbukire kuchita chifundo,
koma analondola wozunzika ndi waumphawi,
ndi wosweka mtima, kuti awaphe.
17 Inde, anakonda kutemberera, ndipo kudamdzera mwini;
sanakondwere nako kudalitsa, ndipo kudamkhalira kutali.
18 Anavalanso temberero ngati malaya,
ndipo lidamlowa m’kati mwake ngati madzi,
ndi ngati mafuta m’mafupa ake.
19 Limkhalire ngati chovala adzikuta nacho,
ndi lamba limene adzimangirira nalo m’chuuno chimangirire.
20 Ichi chikhale mphotho ya otsutsana nane yowapatsa Yehova,
ndi ya iwo akunenera choipa moyo wanga.
21 Koma Inu, Yehova Ambuye,
muchite nane chifukwa cha dzina lanu;
ndilanditseni popeza chifundo chanu ndi chabwino.
22 Pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi,
ndi mtima wanga walaswa m’kati mwanga.
23 Ndamuka ngati mthunzi womka m’tali;
ndiingidwa kwina ndi kwina ngati dzombe.
24 Mabondo anga agwedezeka chifukwa cha kusala;
ndi mnofu wanga waonda posowa mafuta.
25 Ndiwakhaliranso chotonza;
pakundiona apukusa mutu.
26 Ndithandizeni Yehova, Mulungu wanga:
Ndipulumutseni monga mwa chifundo chanu;
27 kuti adziwe kuti ichi ndi dzanja lanu;
kuti Inu Yehova munachichita.
28 Atemberere iwowa, koma mudalitse ndinu;
pakuuka iwowa adzachita manyazi,
koma mtumiki wanu adzakondwera.
29 Otsutsana nane avale manyazi,
nadzikute nacho chisokonezo chao ngati ndi chofunda.
30 Ndidzayamika Yehova kwakukulu pakamwa panga;
ndi pakati pa anthu aunyinji ndidzamlemekeza.
31 Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi,
kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/109-645311000c9cff2c61ddadeadf15563b.mp3?version_id=1068—