Categories
AHEBRI

AHEBRI 2

Yesu Khristu Nkhoswe yathu yakuposa angelo akhoza kumva nafe chifundo

1 Mwa ichi tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.

2 Pakuti ngati mau adalankhulidwa ndiangeloadakhala okhazikika, ndipo cholakwira chilichonse ndi chosamvera chalandira mphotho yobwezera yolungama,

3 tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife;

4 pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.

5 Pakuti sanagonjetsere angelo dziko lilinkudza limene tinenali.

6 Koma wina anachita umboni pena, nati,

Munthu nchiyani kuti mumkumbukira iye?

Kapena mwana wa munthu kuti mucheza naye?

7 Munamchepsa pang’ono ndi angelo,

mudamveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu,

ndipo mudamuika iye woyang’anira ntchito za manja anu;

8 mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake.

Pakuti muja adagonjetsa zonse kwa iye, sanasiyepo kanthu kosamgonjera iye. Koma sitinayambe tsopano apa kuona zonse zimgonjera.

9 Koma timpenya Iye amene adamchepsa pang’ono ndi angelo, ndiye Yesu, chifukwa cha zowawa za imfa, wovala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi chisomo cha Mulungu alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.

10 Pakuti kunamuyenera Iye amene zonse zili chifukwa cha Iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri alowe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa chipulumutso chao mwa zowawa.

11 Pakuti Iye wakuyeretsa ndi iwo akuyeretsedwa achokera onse mwa mmodzi; chifukwa cha ichi alibe manyazi kuwatcha iwo abale.

12 Ndi kuti,

Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga,

pakati paMpingondidzakuimbirani.

13 Ndiponso,

Ndidzamtama Iye.

Ndiponso,

Taonani, Ine ndi ana amene Mulungu anandipatsa.

14 Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi;

15 nakamasule iwo onse amene, chifukwa cha kuopa imfa, m’moyo wao wonse adamangidwa ukapolo.

16 Pakuti ndithu salandira angelo, koma alandira mbeu ya Abrahamu.

17 Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m’zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m’zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.

18 Pakuti popeza adamva zowawa, poyesedwa yekha, akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/2-fc1a794c8b98ac9014c20c24cf8d9571.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *