Mulungu Msungi wokhulupirika wa anthu ake
Nyimbo yokwerera.
1 Ndikweza maso anga kumapiri:
Thandizo langa lidzera kuti?
2 Thandizo langa lidzera kwa Yehova,
wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.
3 Sadzalola phazi lako literereke:
Iye amene akusunga sadzaodzera.
4 Taonani, wakusunga Israele
sadzaodzera kapena kugona.
5 Yehova ndiye wakukusunga;
Yehova ndiye mthunzi wako wa kudzanja lako lamanja.
6 Dzuwa silidzawamba usana,
mwezi sudzakupanda usiku.
7 Yehova adzakusunga kukuchotsera zoipa zilizonse;
adzasunga moyo wako.
8 Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako,
kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/121-fa95c6d1f2abdc05f916ba5667688051.mp3?version_id=1068—