Pemphero la wonyozedwa
Nyimbo yokwerera.
1 Ndikweza maso anga kwa Inu,
kwa Inu wakukhala kumwamba.
2 Taonani, monga maso a anyamata
ayang’anira dzanja la ambuye wao,
monga maso a adzakazi
ayang’anira dzanja la mbuye wao wamkazi:
Momwemo maso athu ayang’anira Yehova Mulungu wathu,
kufikira atichitira chifundo.
3 Mutichitire chifundo, Yehova, mutichitire chifundo;
pakuti takhuta kwambiri ndi mnyozo.
4 Moyo wathu wakhuta ndithu
ndi kuseka kwa iwo osasowa kanthu,
ndi mnyozo wa odzikuza.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/123-3cf70daca6d6cb1ca6b207ff6ebd2c65.mp3?version_id=1068—