Madalitso onse, a m’banja omwe, achokera kwa Mulungu
Nyimbo yokwerera; ya Solomoni.
1 Akapanda kumanga nyumba Yehova,
akuimanga agwiritsa ntchito chabe;
akapanda kusunga mzinda Yehova,
mlonda adikira chabe.
2 Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo,
kudya mkate wosautsa kuupeza;
kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m’tulo.
3 Taonani, ana ndiwo cholowa cha kwa Yehova;
chipatso cha m’mimba ndicho mphotho yake.
4 Ana a ubwana wake wa munthu
akunga mivi m’dzanja lake la chiphona.
5 Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake:
sadzachita manyazi iwo,
pakulankhula nao adani kuchipata.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/127-eeeab4dcd9f3f75aeebe2f4be6f88302.mp3?version_id=1068—