Categories
AHEBRI

AHEBRI 4

1 Chifukwa chake tiope kuti kapena likatsala lonjezano lakulowa mpumulo wake, wina wa inu angaoneke ngati adaliperewera.

2 Pakuti kwa ifenso walalikidwa Uthenga Wabwino, monganso kwa iwo; koma iwowa sanapindule nao mau omvekawo, popeza sanasakanizike ndi chikhulupiriro mwa iwo amene adawamva.

3 Popeza ife amene takhulupirira tilowa mpumulowo, monga momwe ananena,

Monga ndalumbira mu mkwiyo wanga,

ngati adzalowa mpumulo wanga.

Zingakhale ntchitozo zidatsirizika kuyambira kuzika kwa dziko lapansi.

4 Pakuti wanena pena za tsiku lachisanu ndi chiwiri, natero, Ndipo Mulungu anapumula tsiku lachisanu ndi chiwiri, kuleka ntchito zake zonse.

5 Ndipo m’menemonso,

Ngati adzalowa mpumulo wanga.

6 Popeza tsono patsala kuti ena akalowa momwemo, ndi iwo amene Uthenga Wabwino unalalikidwa kwa iwo kale sanalowemo chifukwa cha kusamvera,

7 alangizanso tsiku lina, ndi kunena mu Davide, itapita nthawi yaikulu yakuti, Lero, monga kwanenedwa kale,

Lero ngati mudzamva mau ake,

musaumitse mitima yanu.

8 Pakuti ngati Yoswa akadawapumitsa iwo, sakadalankhula m’tsogolomo za tsiku lina.

9 Momwemo utsalira mpumulo waSabatawa kwa anthu a Mulungu.

10 Pakuti iye amene adalowa mpumulo wake, adapumulanso mwini wake kuntchito zake, monganso Mulungu kuzake za Iye.

11 Chifukwa chake tichite changu cha kulowa mpumulowo, kuti wina angagwe m’chitsanzo chomwe cha kusamvera.

12 Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.

13 Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.

Khristu aposa akulu a ansembe

14 Popeza tsono tili naye Mkulu wa ansembe wamkulu, wopyoza miyamba, Yesu mwana wa Mulungu, tigwiritsitse chivomerezo chathu.

15 Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m’zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.

16 Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/4-3149056aa2f36539013e78c49169a9d9.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *