Alemekeze dzina la Mulungu chifukwa cha zokoma amachitira anthu ake
1 Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma;
pakuti chikondweretsa ichi, chilemekezo chiyenera.
2 Yehova amangaYerusalemu;
asokolotsa otayika a Israele.
3 Achiritsa osweka mtima,
namanga mabala ao.
4 Awerenga nyenyezi momwe zili;
azitcha maina zonsezi.
5 Ambuye wathu ndi wamkulu ndi wa mphamvu zambiri;
nzeru yake njosatha.
6 Yehova agwiriziza ofatsa;
atsitsira oipa pansi.
7 Yamikani Yehova ndi kuthira mang’ombe;
muimbireni Mulungu wathu zomlemekeza pazeze:
8 Amene aphimba thambo ndi mitambo,
amene akonzera mvula nthaka,
amene aphukitsa msipu pamapiri.
9 Amene apatsa zoweta chakudya chao,
ana a khwangwala alikulira.
10 Mphamvu ya kavalo siimkonda:
Sakondwera nayo miyendo ya munthu.
11 Yehova akondwera nao akumuopa Iye,
iwo akuyembekeza chifundo chake.
12 Yerusalemu, lemekezani Yehova;
Ziyoni, lemekezani Mulungu wanu.
13 Popeza analimbitsa mipiringidzo ya zitseko zanu:
Anadalitsa ana anu m’kati mwanu.
14 Ndiye amene akhalitsa malire anu mumtendere;
akukhutitsani ndi tirigu wakucha bwino.
15 Atumiza lamulo lake kudziko lapansi;
mau ake athamanga liwiro.
16 Apatsa chipale chofewa ngati ubweya;
awaza chisanu ngati phulusa.
17 Aponya matalala ake ngati zidutsu:
Adzaima ndani pa kuzizira kwake?
18 Atumiza mau ake nazisungunula;
aombetsa mphepo yake, ayenda madzi ake.
19 Aonetsa mau ake kwa Yakobo;
malemba ake, ndi maweruzo ake kwa Israele.
20 Sanatero nao anthu a mtundu wina;
ndipo za maweruzo ake, sanawadziwe.
Aleluya.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/147-908d9874eb731e84402030f8fb68f978.mp3?version_id=1068—