Categories
AHEBRI

AHEBRI 6

1 Mwa ichi, polekana nao mau a chiyambidwe chaKhristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha pa Mulungu,

2 a chiphunzitso cha ubatizo, a kuika manja, a kuuka kwa akufa, ndi a chiweruziro chosatha.

3 Ndipo ichi tidzachita, akatilola Mulungu.

4 Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yake, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera,

5 nalawa mau okoma a Mulungu, ndi mphamvu ya nthawi ilinkudza,

6 koma anagwa m’chisokero; popeza adzipachikiranso okha Mwana wa Mulungu, namchititsa manyazi poyera.

7 Pakuti nthaka imene idamwa mvula iigwera kawirikawiri, nipatsa therere loyenera iwo amene adailimira, ilandira dalitso lochokera kwa Mulungu:

8 koma ikabala minga ndi mitungwi, itayika; nitsala pang’ono ikadatembereredwa; chitsiriziro chake ndicho kutenthedwa.

9 Koma, okondedwa, takopeka mtima kuti za inu zili zoposa ndi zophatikana chipulumutso, tingakhale titero pakulankhula;

10 pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.

11 Koma tikhumba kuti yense wa inu aonetsere changu chomwechi cholinga kuchiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro;

12 kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.

13 Pakuti pamene Mulungu analonjezana naye Abrahamu, popeza analibe wamkulu woposa kumlumbira, analumbira pa Iye yekha,

14 nati, Kudalitsatu ndidzakudalitsa iwe, ndipo kuchulukitsa ndidzakuchulukitsa iwe.

15 Ndipo potero atapirira analandira lonjezanolo.

16 Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m’chitsutsano chao chilichonse lumbiro litsiriza kutsimikiza.

17 Momwemo Mulungu, pofuna kuonetsera mochulukira kwa olowa a lonjezano kuti chifuniro chake sichisinthika, analowa pakati ndi lumbiro;

18 kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m’mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;

19 chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m’katikati mwa chophimba;

20 m’mene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo laMelkizedeki.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/6-82e75569e42eda650050838c72d7806c.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *