1 Muyeso wonyenga unyansa Yehova;
koma mulingo wamphumphu umsekeretsa.
2 Pakudza kudzikuza padzanso manyazi;
koma nzeru ili ndi odzichepetsa.
3 Kuongoka mtima kwa olungama kuwatsogolera;
koma kukhota kwa achiwembu kudzawaononga.
4 Chuma sichithandiza tsiku la mkwiyo;
koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.
5 Chilungamo cha wangwiro chimaongola njira yake;
koma woipa adzagwa ndi zoipa zake.
6 Chilungamo cha oongoka mtima chidzawapulumutsa;
koma achiwembu adzagwidwa ndi mphulupulu yao.
7 Pomwalira woipa chidikiro chake chionongeka;
chiyembekezo cha uchimo chionongeka.
8 Wolungama apulumuka kuvuto;
woipa nalowa m’malo mwake.
9 Wonyoza Mulungu aononga mnzake ndi m’kamwa mwake;
koma olungama adzapulumuka pakudziwa.
10 Olungama akapeza bwino, mzinda usekera;
nufuula pakuonongeka oipa.
11 Madalitso a olungama akuza mzinda;
koma m’kamwa mwa oipa muupasula.
12 Wopeputsa mnzake asowa nzeru;
koma wozindikira amatonthola.
13 Kazitape woyendayenda amawanditsa zinsinsi;
koma wokhulupirika mtima abisa mau.
14 Popanda upo wanzeru anthu amagwa;
koma pochuluka aphungu pali chipulumutso.
15 Woperekera mlendo chikole adzaphwetekwapo;
koma wakuda chikole akhala ndi mtendere.
16 Mkazi wodekha agwiritsa ulemu;
aukali nagwiritsa chuma.
17 Wachifundo achitira moyo wake zokoma;
koma wankhanza avuta nyama yake.
18 Woipa alandira malipiro onyenga;
koma wofesa chilungamo aonadi mphotho.
19 Wolimbikira chilungamo alandira moyo;
koma wolondola zoipa adzipha yekha.
20 Okhota mtima anyansa Yehova;
koma angwiro m’njira zao amsekeretsa.
21 Zoonadi, wochimwa sadzapulumuka chilango;
koma mbeu ya olungama idzalanditsidwa.
22 Monga chipini chagolide m’mphuno ya nkhumba,
momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.
23 Chifuniro cha olungama chifikitsa zabwino zokha;
koma chiyembekezo cha oipa mkwiyo.
24 Alipo wogawira, nangolemerabe;
aliponso womana chomwe ayenera kupatsa nangosauka.
25 Mtima wa mataya udzalemera;
wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.
26 Womana tirigu anthu amtemberera;
koma madalitso adzakhala pamutu pa wogulitsa.
27 Wopwaira ubwino afunitsa chikondwerero;
koma zoipa zidzamfikira wozilondola.
28 Wokhulupirira chuma chake adzagwa;
koma olungama adzaphuka ngati tsamba.
29 Wovuta banja lake adzalowa m’zomsautsa;
wopusa adzatumikira wanzeru.
30 Chipatso cha wolungama ndi mtengo wa moyo;
ndipo wokola mtima ali wanzeru.
31 Taonani, wolungama adzalandira mphotho kunja kuno;
koposa kotani woipa ndi wochimwa?
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/11-3a2dfc12137683cdafeb18a644d55365.mp3?version_id=1068—