1 Mwana wanzeru amamvera mwambo wa atate;
koma wonyoza samvera chidzudzulo.
2 Munthu adzadya zabwino ndi zipatso za m’kamwa mwake;
koma moyo wa achiwembu udzadya chiwawa.
3 Wogwira pakamwa pake asunga moyo wake;
koma woyasamula milomo yake adzaonongeka.
4 Moyo wa waulesi ukhumba osalandira kanthu;
koma moyo wa akhama udzalemera.
5 Wolungama ada mau onama;
koma woipa anyansa, nadzichititsa manyazi.
6 Chilungamo chitchinjiriza woongoka m’njira;
koma udyo ugwetsa wochimwa.
7 Alipo wodziyesa wolemera, koma alibe kanthu;
alipo wodziyesa wosauka, koma ali ndi chuma chambiri.
8 Chiombolo cha moyo wa munthu ndicho chuma chake;
koma wosauka samva chidzudzulo.
9 Kuunika kwa olungama kukondwa;
koma nyali ya oipa idzazima.
10 Kudzikuza kupikisanitsa;
koma omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru.
11 Chuma cholandiridwa mokangaza chidzachepa;
koma wokundika ndi dzanja adzaona zochuluka.
12 Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima;
koma pakufika chifunirocho ndicho mtengo wa moyo.
13 Wonyoza mau adziononga yekha;
koma woopa malangizo adzalandira mphotho.
14 Malamulo a wanzeru ndiwo kasupe wa moyo,
apatutsa kumisampha ya imfa.
15 Nzeru yabwino ipatsa chisomo;
koma njira ya achiwembu ili makolokoto.
16 Yense wochenjera amachita mwanzeru;
koma wopusa aonetsa utsiru.
17 Mthenga wolakwa umagwa m’zoipa;
koma mtumiki wokhulupirika alamitsa.
18 Wokana mwambo adzasauka nanyozedwa;
koma wolabadira chidzudzulo adzalemekezedwa.
19 Chifuniro chikondweretsa moyo chitachitidwa;
koma kusiya zoipa kunyansa opusa.
20 Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru:
koma mnzao wa opusa adzaphwetekedwa.
21 Zoipa zilondola ochimwa;
koma olungama adzalandira mphotho yabwino.
22 Wabwino asiyira zidzukulu zake cholowa chabwino;
koma wochimwa angosungira wolungama chuma chake.
23 M’kulima kwa osauka muli zakudya zambiri;
koma zinazo zimaonongeka posowa chiweruzo.
24 Wolekerera mwanake osammenya amuda;
koma womkonda amyambize kumlanga.
25 Wolungama adya nakhutitsa moyo wake;
koma mimba ya oipa idzasowa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/13-7e0058e913f39c50a46da6638a98fbd4.mp3?version_id=1068—