Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 14

1 Mkazi yense wanzeru amanga banja lake;

koma wopusa alipasula ndi manja ake.

2 Woyenda moongoka mtima aopa Yehova;

koma wokhota m’njira yake amnyoza.

3 M’kamwa mwa chitsiru muli nthyole ya kudzikuza;

koma milomo ya anzeru idzawasunga.

4 Popanda zoweta modyera muti see;

koma mphamvu ya ng’ombe ichulukitsa phindu.

5 Mboni yokhulupirika siidzanama;

koma mboni yonyenga imalankhula zonama.

6 Wonyoza afunafuna nzeru osaipeza;

koma wozindikira saona vuto m’kuphunzira.

7 Pita pamaso pa munthu wopusa,

sudzazindikira milomo yakudziwa.

8 Nzeru ya wochenjera ndiyo yakuti azindikire njira yake;

koma utsiru wa opusa ndiwo chinyengo.

9 Zitsiru zinyoza kupalamula;

koma mwa oongoka mtima muli chiyanjano.

10 Mtima udziwa kuwawa kwakekwake;

mlendo sadudukira ndi chimwemwe chake.

11 Nyumba ya oipa idzapasuka;

koma hema wa oongoka mtima adzakula.

12 Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka;

koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.

13 Ngakhale m’kuseka mtima uwawa;

ndipo matsiriziro a chiphwete ndi chisoni.

14 Wobwerera m’mbuyo m’mtima adzakhuta njira yake;

koma munthu wabwino adzakhuta za mwa iye yekha.

15 Wachibwana akhulupirira mau onse;

koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.

16 Wanzeru amaopa nasiya zoipa;

koma wopusa amanyada osatekeseka.

17 Wokangaza kukwiya adzachita utsiru;

ndipo munthu wa ziwembu adzadedwa.

18 Achibwana amalandira cholowa cha utsiru;

koma ochenjera amavala nzeru ngati korona.

19 Oipa amagwadira abwino,

ndi ochimwa pa makomo a olungama.

20 Waumphawi adedwa ndi anzake omwe;

koma akukonda wolemera achuluka.

21 Wonyoza anzake achimwa;

koma wochitira osauka chifundo adala.

22 Kodi oganizira zoipa sasochera?

Koma akuganizira zabwino adzalandira chifundo ndi ntheradi.

23 M’ntchito zonse muli phindu;

koma kulankhulalankhula kungopatsa umphawi.

24 Korona wa anzeru ndi chuma chao;

utsiru wa opusa ndiwo utsiru.

25 Mboni yoona imalanditsa miyoyo;

koma wolankhula zonama angonyenga.

26 Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba;

ndipo ana ake adzakhala ndi pothawirapo.

27 Kuopa Yehova ndiko kasupe wa moyo,

kupatutsa kumisampha ya imfa.

28 Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu;

koma popanda anthu kalonga aonongeka.

29 Wosakwiya msanga apambana kumvetsa;

koma wansontho akuza utsiru.

30 Mtima wabwino ndi moyo wa thupi;

koma nsanje ivunditsa mafupa.

31 Wotsendereza aumphawi atonza Mlengi wake;

koma wochitira wosauka chifundo amlemekeza.

32 Wochimwa adzakankhidwa m’kuipa kwake;

koma wolungama akhulupirirabe pomwalira.

33 Nzeru ikhalabe m’mtima wa wozindikira,

nidziwika pakati pa opusa.

34 Chilungamo chikuza mtundu wa anthu;

koma tchimo lichititsa fuko manyazi.

35 Mfumu ikomera mtima kapolo wochita mwanzeru;

koma idzakwiyira wochititsa manyazi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/14-9edb0598af40259cf8f0a0a5776b6b60.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *