Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 18

1 Wopanduka afunafuna chifuniro chake,

nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.

2 Wopusa sakondwera ndi kuzindikira;

koma kungovumbulutsa za m’mtima mwake.

3 Pakudza wamphulupulu padzanso kunyoza;

manyazi natsagana ndi chitonzo.

4 Mau a m’kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya;

kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wodzala.

5 Kukometsa mlandu wa wamphulupulu mwatsankho sikuli kwabwino,

ngakhale kuchitira chetera wolungama.

6 Milomo ya wopusa ifikitsa makangano;

ndipo m’kamwa mwake muputa kukwapulidwa.

7 M’kamwa mwa wopusa mumuononga,

milomo yake ikhala msampha wa moyo wake.

8 Mau akazitape akunga zakudya zolongosoka,

zotsikira m’kati mwa mimba.

9 Wogwira ntchito mwaulesi

ndiye mbale wake wa wosakaza.

10 Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba;

wolungama athamangiramo napulumuka.

11 Chuma cha wolemera ndicho mzinda wake wolimba;

alingalira kuti ndicho khoma lalitali.

12 Mtima wa munthu unyada asanaonongeke;

koma chifatso chitsogolera ulemu.

13 Wobwezera mau asanamvetse apusa,

nadzichititsa manyazi.

14 Mtima wa munthu umlimbitsa alikudwala;

koma ndani angatukule mtima wosweka?

15 Mtima wa wozindikira umaphunzira;

khutu la anzeru lifunitsa kudziwa.

16 Mtulo wa munthu umtsegulira njira,

numfikitsa pamaso pa akulu.

17 Woyamba kudzinenera ayang’anika wolungama;

koma mnzake afika namuululitsa zake zonse.

18 Maere aletsa makangano,

nulekanitsa amphamvu.

19 Kupembedza mbale utamchimwira nkovuta,

kulanda mzinda wolimba nkosavuta;

makangano akunga mipiringidzo ya linga.

20 Mimba ya munthu idzakhuta zipatso za m’kamwa mwake;

iye nadzakhuta phindu la milomo yake.

21 Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo;

wolikonda adzadya zipatso zake.

22 Wopeza mkazi apeza chinthu chabwino;

Yehova amkomera mtima.

23 Wosauka amadandaulira;

koma wolemera ayankha mwaukali.

24 Woyanjana ndi ambiri angodziononga;

koma lilipo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/18-2ffd527be5c96b42d81c856660161173.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *