Categories
AHEBRI

AHEBRI 8

Yesu ali Mkulu wa ansembe wa chipangano chatsopano

1 Koma mutu wa izi tanenazi ndi uwu: Tili naye Mkulu wa ansembe wotere, amene anakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Ukulu mu Kumwamba,

2 Mtumiki wa malo opatulika, ndi wa chihema choona, chimene Ambuye anachimanga, si munthu ai.

3 Pakuti mkulu wa ansembe aliyense aikidwa kupereka mitulo, ndiponso nsembe; potero nkufunika kuti ameneyo akhale nako kanthunso kakupereka.

4 Ndipo Iye akadakhala padziko, sakadakhala konse wansembe, popeza pali iwo akupereka mitulo monga mwa lamulo;

5 amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa m’mene anafuna kupanga chihema: pakuti, Chenjera, ati, uchite zonse monga mwa chitsanzocho chaonetsedwa kwa iwe m’phiri.

6 Koma tsopano Iye walandira chitumikiro chomveka koposa, umonso ali Nkhoswe ya pangano labwino loposa, limene likhazikika pa malonjezano oposa.

7 Pakuti loyamba lija likadakhala lopanda chilema sakadafuna malo a lachiwirilo.

8 Pakuti powatchulira iwo chifukwa, anena,

Taonani, akudza masiku, anena Ambuye,

Ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israele,

ndi nyumba ya Yuda,

9 losati longa pangano ndinalichita ndi makolo ao,

tsikuli ndinawagwira kudzanja iwo kuwatsogolera

atuluke m’dziko la Ejipito;

kuti iwo sanakhalebe m’pangano langa,

ndipo Ine sindinawasamalire iwo, anena Ambuye.

10 Pakuti ili ndi pangano ndidzalipangana ndi nyumba ya Israele,

atapita masiku ajawa, anena Ambuye:

Ndidzapatsa malamulo anga kuwalonga m’nzeru zao,

ndipo pamtima pao ndidzawalemba iwo;

ndipo ndidzawakhalira iwo Mulungu,

ndipo iwo adzandikhalira Ine anthu:

11 Ndipo sadzaphunzitsa yense mfulu mnzake,

ndipo yense mbale wake, ndi kuti, Zindikira Ambuye:

Pakuti onse adzadziwa Ine,

kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu wa iwo.

12 Kuti ndidzachitira chifundo zosalungama zao,

ndipo zoipa zao sindidzazikumbukanso.

13 Pakunena Iye, Latsopano, anagugitsa loyambali. Koma chimene chilinkuguga ndi kusukuluka, chayandikira kukanganuka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/8-929b266e7ccf7e0442c70f84c3911183.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *