Matsoka ndi mavuto a moyo uno
1 Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.
2 Ndipo ndinatama akufa atatha kufa kupambana amoyo omwe alipobe;
3 inde yemwe sanabadwe konse aposa onse awiriwo popeza sanaone ntchito yoipa yochitidwa kunja kuno.
4 Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
5 Chitsiru chimanga manja ake, ndipo chidya nyama yakeyake.
6 Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja awiri oti thoo pali vuto ndi kungosautsa mtima.
7 Pamenepo ndinabwera ndi kupenyera zachabe kunja kuno.
8 Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu.
9 Awiri aposa mmodzi; pakuti ali ndi mphotho yabwino m’ntchito zao.
10 Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzake; koma tsoka wakugwa wopanda womnyamutsa.
11 Ndiponso awiri akagona limodzi afunditsana; koma mmodzi pa yekha kodi adzafunditsidwa bwanji?
12 Ndipo wina akamgonjetsa mmodziyo, awiri adzachilimika; ndipo chingwe cha nkhosi zitatu sichiduka msanga.
13 Mnyamata wosauka ndi wanzeru apambana mfumu yokalamba ndi yopusa, imene sifunanso kulangidwa mwambo.
14 Pakuti atuluka m’nyumba yandende kulowa ufumu; komanso yemwe abadwa m’dziko lake asauka.
15 Ndinapenyera anthu onse amoyo akuyenda kunja kuno, kuti anali ndi mwana, wachiwiri, amene adzalowa m’malo mwake.
16 Anthu onse sawerengeka, ngakhale onsewo anawalamulira; koma amene akudza m’mbuyo sadzakondwera naye. Ichinso ndi chabe ndi chosautsa mtima.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/4-ea0ce4db12a609a9f25f50b4fe08a092.mp3?version_id=1068—