Kumva zowawa nkokoma, nzeru ndi kudziletsa momwemo
1 Mbiri yabwino iposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku lakumwalira liposa tsiku lakubadwa.
2 Kunka kunyumba ya maliro kupambana kunka kunyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse; ndipo omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo.
3 Chisoni chiposa kuseka; pakuti nkhope yakugwa ikonza mtima.
4 Mtima wa anzeru uli m’nyumba ya maliro; koma mtima wa zitsiru uli m’nyumba ya kuseka.
5 Kumva chidzudzulo cha anzeru kupambana kumva nyimbo ya zitsiru.
6 Pakuti kuseka kwa chitsiru kunga minga ilikuthetheka pansi pa mphika; ichinso ndi chabe.
7 Indetu nsautso uyalutsa wanzeru; ndi mtulo uipitsa mtima.
8 Chitsiriziro cha kanthu chiposa chiyambi chake; wofatsa mtima apambana wodzikuza mtima.
9 Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m’chifuwa cha zitsiru.
10 Usanene, Kodi bwanji masiku akale anapambana ano? Pakuti sulikufunsa mwanzeru pamenepo.
11 Nzeru ili yabwino pamodzi ndi cholowa; akuona dzuwa apindula nayo.
12 Pakuti nzeru itchinjiriza monga ndalama zitchinjiriza; koma kudziwa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.
13 Tapenya ntchito ya Mulungu; pakuti ndani akhoza kulungamitsa chomwe iye anachikhotetsa?
14 Tsiku la mwai kondwera, koma tsiku la tsoka lingirira; Mulungu waika ichi pambali pa chinzake, kuti anthu asapeze kanthu ka m’tsogolo mwao.
15 Ndaona zonsezi masiku anga achabe; pali wolungama angofa m’chilungamo chake, ndipo pali woipa angokhalabe ndi moyo m’kuipa kwake.
16 Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziononga wekha?
17 Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa; uferenji nthawi yako isanafike?
18 Kuli kwabwino kugwira ichi; indetu, usachotsepo dzanja lako pakuti yemwe aopa Mulungu adzatuluka monsemo.
19 Nzeru ilimbitsa wanzeru koposa akulu khumi akulamulira m’mzinda.
20 Pakuti kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.
21 Mau onsetu onenedwa usawalabadire; kuti usamve kapolo wako alikukutemberera;
22 pakuti kawirikawiritu mtima wako udziwa kuti nawenso unatemberera ena.
23 Ndayesa zonsezi ndi nzeru; ndinati, Ndidzakhala wanzeru; koma inanditalikira.
24 Chakutali ndi chakuyadi, adzachipeza ndani?
25 Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udyo ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;
26 ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wake ukunga maukonde, manja ake ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wochimwa adzagwidwa naye.
27 Taonani, ichi ndachipeza, ati Mlalikiyo, m’kuphatikiza chinthu china ndi chinzake, ndikazindikire malongosoledwe ao;
28 chomwe moyo wanga uchifuna chifunire, koma osachipezai ndi ichi, mwamuna mmodzi mwa chikwi ndinampezadi, koma mkazitu mwa onsewo sindinampeze.
29 Taonani, ichi chokha ndachipeza kuti Mulungu analenga anthu oongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundumitundu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/7-f7d5b47f5a89cf9f8809f560ca047ea2.mp3?version_id=1068—