Langizo la kumvera mfumu
1 Ndani akunga wanzeru? Ndani adziwa tanthauzo la mau? Nzeru ya munthu iwalitsa nkhope yake, kuduwa kwa nkhope yake ndi kusanduka.
2 Nditi, Sunga mau a mfumu, makamaka m’kulumbira Mulungu.
3 Usakangaze kumchokera; usaumirire kanthu koipa; pakuti iyeyo amachita chomwe chimkonda.
4 Pakuti mau a mfumu ali ndi mphamvu; ndipo ndani anganene kwa iye, Kodi uchita chiyani?
5 Wosunga chilamulo sadzadziwa kanthu koipa; ndipo mtima wa munthu wanzeru udziwa nyengo ndi maweruzo;
6 pakuti kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chiweruzo chake; popeza zoipa za munthu zimchulukira;
7 pakuti sadziwa chimene chidzakhala; pakuti ndani angamuuze nthawi yakuti chidzachitidwa?
8 Kulibe munthu ali ndi mphamvu yolamulira mzimu ndi yakutsekereza mzimu; ngakhale mphamvu tsiku la imfa; munkhondo umo mulibe kumasuka; udyo sudzapulumutsa akuzolowerana nao.
9 Zonsezi ndaziona ndi kuyang’anitsa mtima wanga ntchito zonse zichitidwa pansi pano; nthawi yakuti wina apweteka mnzake pomlamulira.
Woipa salangidwa pakuchita pomwepo; mwina wolungama aona nsautso
10 Ndipo ndinaona oipa alikuikidwa m’manda ndi kupita; ndipo omwe anachita zolungama anachokera kumalo opatulika akumzinda nawaiwala; ichinso ndi chabe.
11 Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yao kuchita zoipa.
12 Angakhale wochimwa achita zoipa zambirimbiri, masiku ake ndi kuchuluka, koma ndidziwitsadi kuti omwe aopa Mulungu naopa pamaso pake adzapeza bwino;
13 koma woipa sadzapeza bwino ngakhale kutanimphitsa masiku ake ngati mthunzi; chifukwa saopa pamaso pa Mulungu.
14 Pali chinthu chachabe chimachitidwa pansi pano; chakuti alipo olungama amene aona zomwe ziyenera ntchito za oipa, ndipo alipo oipa amene aona zomwe ziyenera ntchito za olungama. Ndinati, Ichinso ndi chabe.
15 Pompo ndinatama kusekaseka, pakuti munthu alibe kanthu kabwino pansi pano, koma kudya ndi kumwa, ndi kusekera; ndi kuti zimenezi zikhalebe naye m’vuto lake masiku onse a moyo wake umene Mulungu wampatsa pansi pano.
16 Pompo ndinapereka mtima wanga kudziwa nzeru, ndi kupenya ntchito zichitidwa pansi pano; kuti anthu saona tulo konse ndi maso ao ngakhale usana ngakhale usiku;
17 pamenepo ndinaona ntchito zonse za Mulungu kuti anthu sangalondole ntchito zichitidwa pansi pano; pakuti angakhale munthu ayesetsa kuzifunafuna koma sadzazipeza; indetu ngakhalenso wanzeru akati, ndidziwa, koma adzalephera kuzilondola.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/8-594f57f167273c052efbc8fb9252c95c.mp3?version_id=1068—