Categories
YESAYA

YESAYA 11

Ufumu wa mtendere wa Mesiya

1 Ndipo padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese, ndi nthambi yotuluka m’mizu yake idzabala zipatso;

2 Ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova;

3 ndipo adzakondwera nako kumuopa Yehova, ndipo sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera:

4 koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m’dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.

5 Ndipo chilungamo chidzakhala mpango wa m’chuuno mwake, ndi chikhulupiriko chidzakhala mpango wa pa zimpso zake.

6 Mmbulu udzakhala pamodzi ndimwanawankhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwanawambuzi; ndipo mwanawang’ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera.

7 Ndipo ng’ombe yaikazi ndi chilombo zidzadya pamodzi; ndipo ana ao aang’ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng’ombe.

8 Ndipo mwana wakuyamwa adzasewera pa una wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lake m’funkha la mphiri.

9 Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzaza ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.

10 Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Yese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu,amitunduadzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.

11 Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kachiwiri ndi dzanja lake anthu ake otsala ochokera ku Asiriya, ndi ku Ejipito, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m’nyanja.

12 Ndipo Iye adzaimika mbendera ya amitundu, ndipo adzasonkhanitsa oingitsidwa a Israele, namema obalalika a Yuda, kuchokera kumadera anai a dziko lapansi.

13 Ndipo nsanje ya Efuremu idzachoka, ndi iwo amene avuta Yuda adzadulidwa; Efuremu sachitira nsanje Yuda, ndi Yuda sachitira nsanje Efuremu.

14 Ndipo adzagudukira mapewa a Afilisti kumadzulo; pamodzi adzafunkha ana a kum’mawa; adzatambasula dzanja lao pa Edomu ndi pa Mowabu; ndipo ana a Amoni adzawamvera.

15 Ndipo Yehova adzaononga ndithu bondo la nyanja ya Ejipito; ndipo ndi mphepo yake yopsereza adzagwedeza dzanja lake pa Mtsinje, ndipo adzaimenya ikhale mphaluka zisanu ndi ziwiri, nadzaolotsa anthu pansi pouma.

16 Ndipo padzakhala khwalala la anthu ake otsala ochokera ku Asiriya; monga lija la Israele tsiku lokwera iwo kutuluka m’dziko la Ejipito.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/11-cf74500b4ccc87939f4e1bda5835d52b.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *