Aneneratu za kuonongeka kwa Mowabu
1 Katundu wa Mowabu. Pakuti usiku umodzi Ari wa ku Mowabu wapasuka, nakhala chabe; usiku umodzi Kiri wa Mowabu wapasuka, nakhala chabe.
2 Akwera ku Kachisi, ndi ku Diboni, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Mowabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndevu zonse zametedwa.
3 M’makwalala mwao adzimangira chiguduli m’chuuno, pamwamba pa nyumba zao, ndi m’malo a mabwalo ao, yense akuwa, naliritsa kwambiri.
4 Ndi Hesiboni afuula zolimba, ndi Eleyale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; chifukwa chake amuna ankhondo a Mowabu afuula zolimba; moyo wake wanthunthumira m’kati mwake.
5 Mtima wanga ufuula chifukwa cha Mowabu: akulu ake athawira ku Zowari, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa chikweza cha Luhiti akwera alikulira, pakuti m’njira ya Horonaimu akweza mfuu wa chionongeko.
6 Pakuti pamadzi a Nimurimu padzakhala mabwinja; popeza udzu wafota, msipu watha.
7 Chifukwa chake zochuluka adazipeza, ndi zosungidwa zao adzazitenga kunka nazo kumtsinje wa mabango.
8 Pakuti kulira kwamveka kuzungulira malire a Mowabu; kukuwa kwake kwafikira ku Egilaimu, ndi kukuwa kwake kwafikira ku Beerelimu.
9 Pakuti madzi a Diboni adzala mwazi; pakuti ndidzatengera zina pa Diboni, mkango pa iye amene anapulumuka ku Mowabu, ndi pa otsala a m’dziko.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/15-bed74698019bcf4fe35210360f290f02.mp3?version_id=1068—