Aneneratu za Damasiko ndi Efuremu
1 Katundu wa Damasiko. Taonani, Damasiko wachotsedwa usakhalenso mzinda, ndimo udzangokhala muunda wopasulidwa.
2 Mizinda ya Aroere yasiyidwa; idzakhala ya zoweta zogona pansi, opanda woziopsa.
3 Ku Efuremu sikudzakhalanso linga, ngakhale ufumu ku Damasiko, ngakhale otsala kwa Aramu; iwo adzakhala ngati ulemerero wa ana a Israele, ati Yehova wa makamu.
4 Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti ulemerero wa Yakobo udzakhala wopyapyala, ndi kunenepa kwa thupi lake kudzaonda.
5 Ndipo padzakhala ngati wamasika alikumweta tirigu wosacheka, ndi dzanja lake lilikudula ngala; inde padzakhala ngati pamene wina akunkha ngala m’chigwa cha Refaimu.
6 Koma mudzasiyidwa m’menemo khunkha, monga ngati kugwedeza kwake kwa mtengo waazitona, zipatso ziwiri pena zitatu m’nsonga ya nthambi yosomphoka, zinai pena zisanu m’nthambi za kunthemba, za mtengo wobalitsa, ati Yehova, Mulungu wa Israele.
7 Tsiku limenelo munthu adzayang’ana kwa Mlengi wake, ndipo maso ake adzalemekeza Woyera wa Israele.
8 Ndipo iye sadzayang’ana pa maguwa a nsembe, ntchito ya manja ake, ngakhale kulemekeza chimene anachipanga ndi zala zake, ngakhale zifanizo pena mafano a dzuwa.
9 Tsiku limenelo mizinda yake yolimba idzakhala ngati mabwinja a m’nkhalango, ndi a pansonga paphiri, osiyidwa pamaso pa ana a Israele; ndipo padzakhala bwinja.
10 Chifukwa iwe waiwala Mulungu wa chipulumutso chako, sunakumbukire thanthwe la mphamvu zako; chifukwa chake iwe waoka mitengo yokondweretsa, waokapo zipinjiri zachilendo;
11 tsiku lako looka uzingapo mpanda, nuphukitsa mbeu zako m’mawa mwake; mulu wa masika udzaoneka tsiku lakulira ndi la chisoni chothetsa nzeru.
Aneneratu za kufafanizika kwa nkhondo ya Asiriya
12 Ha, phokoso la mitundu yambiri ya anthu ambiri, amene afuula ngati kukukuma kwa nyanja; ndi kuthamanga kwaamitundu, akuthamanga ngati kuthamanga kwa madzi amphamvu!
13 Mitundu ya anthu idzathamanga ngati kuthamanga kwa madzi ambirimbiri; koma Iye adzawadzudzula, ndipo iwo adzathawira patali, nadzapirikitsidwa monga mankhusu a pamapiri patsogolo pa mphepo, ndi monga fumbi lokwetera patsogolo pa mkuntho wa mphepo.
14 Pa nthawi ya madzulo, taonani kuopsa; kusanache, iwo palibe. Ili ndi gawo la iwo amene atifunkha ndi ichi chiwagwera omwe alanda zathu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/17-efdb277ec5798408a0aff2d05bef1929.mp3?version_id=1068—