Categories
YESAYA

YESAYA 26

Nyimbo yakulemekeza kutchinjiriza kwa Yehova

1 Tsiku limenelo adzaimba nyimbo imeneyi m’dziko la Yuda, Ife tili ndi mzinda wolimba; Iye adzaika chipulumutso chikhale machemba ndi malinga.

2 Tsegulani pazipata, kuti mtundu wolungama, umene uchita zoonadi, ulowemo.

3 Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu.

4 Khulupirirani Yehova nthawi zamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire.

5 Chifukwa Iye watsitsira pansi iwo amene anakhala pamwamba, mzinda wa pamsanje; Iye wautsitsa, wautsitsira pansi; waugwetsa pansi pa fumbi.

6 Phazi lidzaupondereza pansi; ngakhale mapazi a aumphawi, ndi mapondedwe a osowa.

7 Njira ya wolungama ili njira yoongoka; Inu amene muli woongoka, mukonza njira ya wolungama.

8 Inde m’njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi chikumbukiro chanu.

9 Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali padziko lapansi, okhala m’dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.

10 Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo; m’dziko la machitidwe oongoka, iye adzangochimwa, sadzaona chifumu cha Yehova.

11 Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona changu chanu cha kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamaliza adani anu.

12 Yehova, mudzatikhazikitsira mtendere; pakuti mwatigwirira ntchito zathu zonse.

13 Yehova Mulungu wathu, pamodzi ndi Inu Ambuye ena adatilamulira ife; koma mwa Inu nokha tidzatchula dzina lanu.

14 Iwo afa, atha, sadzakhalanso ndi moyo; ali mizimu, sadzauka; chifukwa chake Inu munawazonda, ndi kuwaononga, mwathetsa chikumbukiro chao chonse.

15 Mwachulukitsa mtundu, Yehova, mwachulukitsa mtundu; Inu mwalemekezeka, mwakuza malire onse a dziko.

16 Yehova, iwo adza kwa Inu movutika, iwo anathira pemphero, muja munalikuwalanga.

17 Monga ngati mkazi wokhala ndi pakati, amene nthawi yake yakubala yayandikira, amva zopweteka, ndi kufuula m’zowawa zake; momwemo takhala ife pamaso panu, Yehova.

18 Ife tinali ndi pakati, ife tinamva zopweteka, tafanana ngati tabala mphepo; sitinachite chipulumutso chilichonse padziko lapansi; ngakhale okhala m’dziko lapansi sanagwe.

19 Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m’fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.

20 Idzani, anthu anga, lowani m’zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita.

21 Pakuti taonani, Yehova adza kuchokera kumalo ake kudzazonda okhala padziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao; dziko lidzavumbulutsa mwazi wake, ndipo silidzavundikiranso ophedwa ake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/26-3ec228fc2df11ddca7bcd007701d7186.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *