Categories
YESAYA

YESAYA 27

Munda wampesa wa Yehova

1 Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lake lolimba ndi lalikulu ndi lamphamvu adzalangaLeviyataninjoka yothamanga, ndi Leviyatani njoka yopindikapindika; nadzapha ching’ona chimene chili m’nyanja.

2 Tsiku limenelo: munda wa mphesa wavinyo, imbani inu za uwo.

3 Ine Yehova ndiusunga uwo; ndidzauthirira madzi nthawi zonse; ndidzausunga usiku ndi usana, kuti angauipse.

4 Ndilibe ukali; ndani adzalimbanitsa lunguzi ndi minga ndi Ine kunkhondo? Ndiziponde ndizitenthe pamodzi.

5 Kapena mlekeni, agwire mphamvu zanga, nachite nane mtendere; inde, achite nane mtendere.

6 M’mibadwo ikudzayo Yakobo adzamera mizu; Israele adzaphuka ndi kuchita mphundu; ndipo iwo adzadzaza ndi zipatso padziko lonse lapansi.

7 Kodi Mulungu wakantha Yakobo, monga umo anawakanthira akumkanthawo? Kapena kodi iye waphedwa malinga ndi kuphedwa kwa iwo amene anaphedwa ndi iye?

8 Munalimbana naye pang’ono, pamene munamchotsa; wamchotsa iye kuomba kwake kolimba tsiku la mphepo yamlumbanyanja.

9 Chifukwa chake, mwa ichi choipa cha Yakobo chidzafafanizidwa, ndipo ichi ndi chipatso chonse chakuchotsa tchimo lake; pamene iye adzayesa miyala yonse ya guwa la nsembe, ngati miyala yanjeresa yoswekasweka, zifanizo ndi mafano a dzuwa sizidzaukanso konse.

10 Pakuti mzinda wotchingidwa uli pa wokha, mokhalamo mwa bwinja, ndi mosiyidwa ngati chipululu; mwanawang’ombe adzadya kumeneko, nadzagonako pansi, nadzamaliza nthambi zake.

11 Ponyala nthambi zake zidzathyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; chifukwa chake Iye amene anawalenga sadzawachitira chisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.

12 Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Yehova adzaomba tirigu wake, kuchokera madzi a nyanja, kufikira kumtsinje wa Ejipito, ndipo mudzakunkhidwa mmodzi, inu ana a Israele.

13 Ndipo padzakhala tsiku limenelo, lipenga lalikulu lidzaombedwa; ndipo adzafika omwe akadatayika m’dziko la Asiriya, ndi opirikitsidwa a m’dziko la Ejipito; ndipo adzapembedza Yehova m’phiri lopatulika la paYerusalemu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/27-b66afe371a3df3f93dc9b0dbf015b481.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *