Aneneratu za kulangidwa kwa Yuda wosakhulupirika, komanso za chipulumutso chake
1 Eya Ariyele, Ariyele, mzinda umene Davide anamangapo zithando! Onjezerani chaka ndi chaka; maphwando afikenso;
2 pamenepo ndidzasautsa Ariyele, ndipo padzakhala maliro ndi kulira; koma iye adzakhala kwa Ine monga Ariyele.
3 Ndipo ndidzamanga zithando kuzungulira iwe ponse, ndipo ndidzamanga linga ndi kuunjika miulu yakumenyanirana ndi iwe.
4 Ndipo iwe udzagwetsedwa pansi, nudzanena uli pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala pansi kotuluka m’fumbi; ndi mau ako adzakhala ngati a wina amene ali ndi mzimu wobwebweta, kuchokera pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala konong’ona kochokera m’fumbi.
5 Koma khamu la achilendo ako lidzafanana ndi fumbi losalala, ndi khamu la oopsa lidzakhala monga mungu wochokachoka; inde kudzaoneka modzidzimuka dzidzidzi.
6 Ndipo Yehova wa makamu adzamzonda ndi bingu, ndi chivomezi, ndi mkokomo waukulu, kamvulumvulu, ndi mkuntho, ndi lawi la moto wonyambita.
7 Ndipo khamu la mitundu yonse yomenyana ndi Ariyele, ngakhale yonse yomenyana naye ndi linga lake, ndi kumsautsa idzafanana ndi loto, masomphenya a usiku.
8 Ndipo kudzafanana ndi munthu wanjala, pamene alota, ndipo, taonani, akudya; koma auka, ndipo m’kati mwake muli zii; kapena monga munthu waludzu pamene alota, ndipo taonani, akumwa; koma auka ndipo taonani walefuka, ndipo m’kati mwake muli gwaa; momwemo lidzakhala khamu la mitundu yonse yomenyana ndi phiri laZiyoni.
9 Khalani ndi kudabwa; sangalalani ndi kukhala akhungu; iwo aledzera, koma si ndi vinyo, ali dzandidzandi; koma si ndi chakumwa chaukali.
10 Pakuti Yehova watsanulira pa inu mzimu wa tulo togonetsa, natseka maso anu, ndiwo aneneri; naphimba mitu yanu, ndiwo alauli.
11 Ndipo masomphenya onse akusandukirani mau a m’buku limatidwa ndi phula, limene anthu amapereka kwa wina wodziwa kuwerenga, nati, Werengani umu; koma ati, Sindingathe, chifukwa lamatidwa ndi phula;
12 ndipo buku laperekedwa kwa wosadziwa kuwerenga, ndi kuti, Werengani umu; koma ati, Ine sindinaphunzire.
13 Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m’kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;
14 chifukwa chake, taonani, ndidzachitanso mwa anthu awa ntchito yodabwitsa, ngakhale ntchito yodabwitsa ndi yozizwitsa; ndipo nzeru ya anthu ao anzeru idzatha, ndi luntha la anthu ao ozindikira lidzabisika.
15 Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wao, ndi ntchito zao zili mumdima, ndipo amati ndani ationa ife? Ndani atidziwa ife?
16 Ozolitsa inu! Kodi woumba adzayesedwa ngati dothi; kodi chinthu chopangidwa chinganene za iye amene anachipanga, Iye sanandipange ine konse; kapena kodi chinthu choumbidwa chinganene za iye amene anachiumba, Iye alibe nzeru?
17 Kodi sikatsala kamphindi kakang’ono, ndipo Lebanoni adzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango?
18 Ndipo tsiku limenelo gonthi adzamva mau a m’buku, ndi maso akhungu adzaona potuluka m’zoziya ndi mumdima.
19 Ofatsanso kukondwa kwao kudzachuluka mwa Yehova, ndi aumphawi a mwa anthu adzakondwerera mwa Woyera wa Israele.
20 Pakuti woopsa wagoma, ndi wonyoza watha, ndi onse odikira zolakwa alikhidwa;
21 amene apalamulitsa munthu mlandu, namtchera msampha iye amene adzudzula pachipata, nambweza wolungama ndi chinthu chachabe.
22 Chifukwa chake Yehova amene anaombola Abrahamu, atero za banja la Yakobo: Yakobo sadzakhala ndi manyazi tsopano, ngakhale nkhope yake tsopano sidzagwa.
23 Koma pamene iye aona ana ake, ntchito ya manja anga, pakati pa iye, iwo adzayeretsa dzina langa; inde, iwo adzayeretsa Woyera wa Yakobo, nadzaopa Mulungu wa Israele.
24 Iwonso osochera mumzimu adzadziwa luntha, ndi iwo amene ang’ung’udza adzaphunzitsidwa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/29-f9e058f7943a19467d09b4447a8c5db4.mp3?version_id=1068—