Adani a anthu a Mulungu adzapasuka; Yerusalemu adzabwezedwa ulemu
1 Tsoka kwa iwe amene usakaza, chinkana sunasakazidwe; nupangira chiwembu, chinkana sanakupangire iwe chiwembu! Utatha kusakaza, iwe udzasakazidwa; ndipo utatha kupangira chiwembu, iwo adzakupangira iwe chiwembu.
2 Inu Yehova, mutikomere ife mtima; ife talindira Inu; mukhale dzanja lathu m’mawa ndi m’mawa, chipulumutso chathunso m’nthawi ya mavuto.
3 Pa mau a phokoso mitundu ya anthu yathawa; ponyamuka iweamitunduabalalika.
4 Ndipo zofunkha zanu zidzasonkhanitsidwa, monga ziwala zisonkhana; monga dzombe atumpha, iwo adzatumpha pa izo.
5 Yehova wakwezedwa; pakuti akhala kumwamba; Iye wadzazaZiyonindi chiweruzo ndi chilungamo.
6 Ndipo kudzakhala chilimbiko m’nthawi zako, chipulumutso chambiri, nzeru ndi kudziwa; kuopa kwa Yehova ndiko chuma chake.
7 Taonani, olimba mtima ao angofuula kunja, mithenga ya mtendere ilira kowawa.
8 Njira zamakwalala zikufa, kulibe woyendamo; Asiriya wathyolachipangano, wanyoza mizinda, sasamalira anthu.
9 Dziko lirira maliro ndi kulefuka; Lebanoni ali ndi manyazi, nafota; Saroni afanana ndi chipululu; pa Basani ndi Karimele papukutika.
10 Tsopano ndidzauka, ati Yehova; tsopano ndidzanyamuka, tsopano ndidzakwezedwa.
11 Inu mudzatenga pakati ndi mungu, mudzabala ziputu; mpweya wanu ndi moto umene udzakumalizani inu.
12 Ndipo mitundu ya anthu idzanga potentha miyala yanjeresa; monga minga yodulidwa, nitenthedwa ndi moto.
13 Imvani inu amene muli kutali, chimene ndachita ndi inu; amene muli pafupi, vomerezani mphamvu zanga.
14 Ochimwa a mu Ziyoni ali ndi mantha, kunthunthumira kwadzidzimutsa anthu opanda Mulungu. Ndani mwa ife adzakhala ndi moto wakunyeketsa? Ndani mwa ife adzakhala ndi zotentha zachikhalire?
15 Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ake kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ake kusamva za mwazi, natsinzina maso ake kusayang’ana choipa;
16 iye adzakhala pamsanje; malo ake ochinjikiza adzakhala malinga amiyala; chakudya chake chidzapatsidwa kwa iye; madzi ake adzakhala chikhalire.
17 Maso ako adzaona mfumu m’kukongola kwake; iwo adzaona dziko lakutali.
18 Mtima wako udzaganizira zoopsa; mlembi ali kuti? Ali kuti iye amene anayesa msonkho? Ali kuti iye amene anawerenga nsanja?
19 Iwe sudzaona anthu aukali, anthu a mau anthulu, amene iwe sungazindikire; a lilime lachibwibwi, limene iwe sungalimve.
20 Tayang’ana pa Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zathu; maso ako adzaona, Yerusalemu malo a phee, chihema chimene sichidzasunthidwa, zichiri zake sizidzazulidwa konse, zingwe zake sizidzadulidwa.
21 Koma pamenepo Yehova adzakhala ndi ife mu ulemerero, malo a nyanja zachitando ndi mitsinje; m’menemo ngalawa sizidzayenda ndi ngombo, ngakhale zombo zazikulu sizidzapita pamenepo.
22 Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.
23 Zingwe zako za ngalawa zamasulidwa; sizinathe kulimbitsa patsinde pa mlongoti wake, sizinathe kufutukula matanga; pamenepo ndipo cholanda chachikulu, chofunkha chinagawanidwa; wopunduka nafumfula.
24 Ndipo wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala; anthu okhala m’menemo, adzakhululukidwa mphulupulu zao.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ISA/33-3b2e1f19cb8ad1b3adf3c72684cfa257.mp3?version_id=1068—